Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo...

14

Transcript of Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo...

Page 1: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga
Page 2: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

2 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

ZamkatimuKukonzekera ukwati

Kudziteteza ku HIV

Moyo wa m’banja latsopano

Kukhala a thanzi

Kusangalala

Kulera

Kukonzekera mwana

Kuyembekezera

Kupita ku sikelo ya amayi

Kupewa malungo

Kudziwa zizindikiro zoopsa za pathupi

Kukonzekera kubereka

Kubereka

Kusamalira mwana wa khanda

Kadyedwe ka mayi ndi mwana wakhanda

Kusamalira mwana akamakula

Kuteteza mwana ndi banja ku matenda

Kudziwa zizindikiro zoopsa kwa mwana

Katemera

3

3

4

5

5

6

6

7

8

8

9

9

10

10

11

12

12

12

13

Page 3: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

3 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

Mele ndi Joni anapanga ganizo lokayezetsa HIV pamodzi ndipo anakambirana zotsatira.

Analonjezana kukhala okhulupirika ndi kusunga banja lawo.

Anakambirananso za mdulidwe wa abambo umene ukhoza kukhala ndi zotsatira zabwino kwa banja lawo monga kuchepetsa chiopsezo chotenga kachirombo ka HIV komanso khansa ya khomo la chibelekero cha mayi.

Banja losangalala limayamba ndi ubwenzi wabwino, kukhulupirika ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana.Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga izi:• Kodi malingaliro athu ndi otani pa moyo wathu

wa m’banja?• Tingatani kuti tidzisangalatsana?• Tingakonzekere bwanji pa nkhani ya maphunziro

athu ndi ntchito?• Tidzasunga ndi kugwiritsa ntchito bwanji

ndalama zathu?• Maganizo athu pa zachipembedzo ndi otani?• Kodi makhalidwe athu akhale otani?• Abale ndi alongo amene ali oyenera kwa ife ndi

ati?• Kodi ku mabanja athu kuli mbiri ya matenda ena

alionse?• Timafuna kudzakhala ndi ana angati ndipo liti?• Tizakhala bwanji ndi moyo wa thanzi?

Kukonzekera ukwati

Ndimakukonda ndi kukukhulupilira. Tikhale athanzi ndi okhulupirika

kwa wina ndi mzake.

Ndimakukonda ndi kukukhulupilira. Tiye tikayezetse

limodzi ka chirombo ka HIV.

Kudziteteza ku HIV

Page 4: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

4 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

Mele ndi Joni pano amanga ukwati. Zosangalatsa! Njira zina zimene amatsata powonetsetsa kuti banja lawo likhale losangalala ndi la mphamvu ndi izi:

• Nthawi zonse amalankhulana mwa ulemu, mwachilungamo ndi mwansangala. Izi zimafuna kuphunzirana, kumvetsetsana ndi kupilirana.

• Joni amaonetsa chikondi chake kwa Mele pomuuza ndi kumuchitira zinthu zing’onozing’ono ndi zina zikuluzikulu monga kugawana ntchito za pakhomo, kuyendera limodzi ndi zina zotere.

• Amasangalala ndi kuchita zinthu limodzi.

• Amasamala matupi awo pochita ukhondo, kudya bwino, kulimbitsa thupi ndi kukhala omasuka m’maganizo.

• Mele ndi Joni amasangalatsidwa ndi nyumba yawo yaing’ono bwino ndi yaukhondo ndipo akukhala motakasuka asanayambe kuganiza zokhala ndi ana.

Moyo wa m’banja latsopano

Page 5: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

5 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

1. Zokhutitsa: Zakudyazi zimapereka mphamvu komanso kuthandiza kukuza thupi. Izi ndi zakudya monga nsima, mapira, mawere, chimanga, chinangwa, mbatata ndi nthochi yophika.

2. Zanyama: Izi zimathandiza kuti munthu akule komanso zimapereka timichere ta mthupi tothandiza pokula. Zakudyazi ndi monga nyama, mazira, mkaka, nsomba, ngumbi ndi mbalame.

3. Zamasamba: Zili ndi timichere ta mthupi, madzi ndi zina zothandiza kuti chakudya chigayike bwino. Izi ndi zakudya ngati bonongwe, chisoso, khwanya, nkhwani, kholowa, repu, mpiru, kamganje, karoti,

Mele ndi Joni amakonda kuonera masewera a mpira, kuvina, kuseka ndi kusangalala ndi anzawo. Nthawi zina amamwa mowa pang’ono koma amadziwa mulingo wawo.

Kumwa mowa mowonjeza kumabweretsa mavuto. Pozindikira izi, Mele ndi Joni amamwa pang’ono. Nthawi zina samamwa kumene.

Kukhala ndi thanziKuti akhale ndi thanzi, Mele ndi Joni amadya zakudya za magulu asanu ndi limodzi (6) zili m’musizi:

Kusangalala

mabilingano, maungu ndi tomato.

4. Zamafuta: Zimapereka mafuta othandiza kuti thupi likule motakasuka. Izi ndi zakudya ngati soya, mtedza, mapeyala, mafuta ophikira, mkaka ndi zakudya zina zopangidwa kuchokera ku mkaka.

5. Zipatso: Zimapereka mphamvu, timichere ta m’thupi ndi madzi. Izi zimathandiza kuti thupi likule bwino komanso lithe kupewa matenda.Izi ndi zakudya monga mango, mandalena, malalanje, mapapaya, magwafa, nthochi, nanazi ndi bwemba.

6. Zanyemba: Zakudyazi zimathandiza kuti munthu akule bwino. Izi ndi zakudya ngati mtedza, soya, nyemba, nsawawa, khobwe, nzama ndi nandolo. Soya ndi nyemba zimathandizanso kupereka mphamvu m’thupi. Soya ndi mtedza zimakhalanso ndi mafuta omwe amathandiza thupi kukula motakasuka.

Page 6: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

6 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

Mele ndi Joni akufuna kukhala ndi nthawi yokwanira yosangalala ngati banja. Sakufuna kukhala ndi ana mwamsanga. Akufuna adikire kaye. Ngakhale malume a Joni ndi azakhali a Mele akuwaumiriza kuti awapatse zidzukulu, Joni amamuthandiza Mele muchisankho chawo choti adikire kaye.

Joni ndi Mele anasankha kulera chifukwa:

• Akufuna kudzakhala ndi mwana pokhapokha atakonzeka.

• Banja laling’ono ndi losavuta kusamala.

• Kubereka pafupipafupi kukhoza kupereka chiopsezo kwa Mele chifukwa akhoza kukhala ndi magazi operewera m’thupi komanso chitetezo chotsika.

• Kulera kuwathandiza kupanga chisankho pa mfundo izi:

- Ndi liti lomwe tikufuna kudzakhala ndi ana?

Tsopano Mele ndi Joni ndiokonzeka kukhala ndi mwana. Iwo apita ku chipatala kukayankhula ndi azaumoyo. Wazaumoyo walangiza Mele ndi Joni kuti akuyenera kuyezetsa kaye Mele asanatenge pathupi.

Mwa zina, kuyezetsa magazi kudzawathandiza kudziwa izi:

• Ngati ali ndi kachirombo ka HIV kapena matenda ena opatsirana pogonana.

• Ngati Mele ali ndi magazi okwanira.

Kupatula kuyezetsa magazi, wa zaumoyo wati amuyezanso Mele kuti awone ngati alibe mavuto aliwonse omwe angabweretse chiopsezo pa nthawi yoyembekezera komanso yobereka.

Kulera

- Tidzakhala ndi ana angati?

- Tikabereka, padzidzatenga nthawi yaitali bwanji tisanaberekenso mwana wina?

- Tidzasiya liti kubereka?

Aganiza zopita ku chipatala kuti azaumoyo akawathandize kusankha njira yowayenelera.

Kukonzekera mwana

Zonse zilibwino ndipo wa zaumoyo wathandiza Mele ndi Joni kusiya njira yolelera yomwe akugwiritsa ntchito. Mele tsopano akhoza kutenga pathupi.

Page 7: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

7 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

Kuyembekezera

1. Mele ndi Joni anapita ku chipatala komwe anakatsimikiza kuti ndioyembekezera komanso anakalandira chithandizo choyenera.

2. Mele ayenera kupitiriza kudya zakudya za magulu asanu ndi limodzi (6). Akudziwa kuti mayi amayenera kudya bwino ali ndi pa thupi kuti mwana amene akuyembekezerayo akule ndi thanzi komanso nzeru. Akudziwanso kuti mwana akanyentchera asanabadwe komanso ali wamn’gono, amakhala ndi mavuto aakulu osakonzeka monga umbuli komanso kusokonekera kwa ubongo.

3. Mele ndi Joni akufuna kukonzekera bwino kubereka. Akufuna adziwe zizindikiro zoopsya za mayi pa nthawi imene ali ndi pakati komanso pa nthawi yobereka.

4. Mele ndi Joni anamvapo kuti malungo ndi oopsya kwa mayi woyembekezera. Akufuna adziwe m’mene angadzitetezere ku malungo pa nthawiyi.

4. Joni akutenga mbali powonetsetsa kuti Mele ali ndi thanzi pa nthawi imene akuyembekezera. Amaonetsetsa kuti Mele akudya zakudya za magulu, amamuperekeza ku sikelo komanso kumukumbutsa za malangizo omwe alandira ku chipatala.

Mele ndi Joni ndi osangalala pozindikira kuti posachedwapa akhala makolo. Ichi chikhala chiyambi cha moyo wina watsopano. Awiriwa akufuna kuonetsetsa kuti Mele ndi mwana yemwe akuyembekezerayo ndi athanzi.

Page 8: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

8 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

Wa zaumoyo walangiza Mele ndi Joni kuti ayenera kupita ku sikelo kanayi (4) pa nthawi imene akuyembekezera.• Koyamba: Akangodziwa kuti ali ndi pathupi

(miyezi itatu yoyambilira).• Kachiwiri: Pakati pa mwezi wa chisanu (5) ndi

wa sikisi (6).• Kachitatu: Pakati pa mwezi wa seveni (7) ndi

wa eyiti (8).• Kachinayi: Kumayambiliro kwa mwezi wa

chisanu ndi chinayi (9).Popita ku sikelo mwa ndondomeko, Mele adzakhala ndi mwai:

• Joni amakumbutsa Mele kuti usiku uliwonse adzigona mu neti yonyikidwa m’mankhwala opha udzudzu.

• Mele ndi Joni amapita ku chipatala komwe Mele amalandira mankhwala oteteza ku malungo. Wa zaumoyo anawalangiza kuti Mele akuyenera kumwa mankwalawa katatu pamene akuyembekezera.

Kupita ku sikelo ya amayi

Akapita ku sikelo, Mele ndi Joni amamvetsera bwino malangizo onse kuti adzikakumbutsana zomwe amva.

Kupewa malungoMalungo ndi oopsya kwa wina aliyense makamaka kwa amayi oyembekezera.

• Wolandira katemera wa amayi.• Wolandira mankhwala ndi ma vitamini omwe amaonjezera magazi ndi kuthandiza

kuti mwana akule bwino.• Kuyezetsa kachirombo ka HIV ndi matenda ena.• Kuyezetsa ngati Mele ndi mwana wake ali bwino.

Page 9: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

9 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

Mele anauzidwa kuti ngati akumva kapena kuona zina mwa zizindikiro izi apite ku chipatala mwamsanga:• Kutopa kwambiri kapena kupuma movutika.• Kuyera m’manja kapena m’maso.• Kutupa miyendo, manja kapena nkhope.• Kuphwanya m’thupi, kupweteka mutu, kuchita

chizungulire kapena kusanza kangapo pa tsiku.• Kutuluka ukazi.• Kukomoka.• Kumva kupweteka potaya madzi.• Kupweteka kwambiri mkati mwa chibelekero.• Mwana kusiya kusuntha m’mimba.

• Mele ndi Joni anafunsa wa zaumoyo tsiku lomwe adzabereke.

• Amasunga ndalama zodzagwiritsa ntchito pa nthawi yobereka.

• Amaguliratu zinthu zodzafunika pa nthawi yobereka ngakhalenso ngati patachitika zadzidzidzi.

• Joni wakonzekeratu mayendedwe odzapita ku chipatala akadzaona zizindikiro zobereka. Ayenera kukhala ndi mayendedwe odalirika.

• Chifukwa chakuti chipatala chomwe adzabelekere chili kutali, akukonzekera kudzapita ku malo odikilira ku chipatala konko kwa masabata awiri nthawi yobelekera isanakwane.

Kudziwa zizindikiro zoopsa za pathupi

Kukonzekera kubereka

Ngakhale Mele ndi Joni akonzekera bwino zakubadwa kwa mwana, wa zaumoyo adawafotokozera kuti ngati mwadzidzidzi ataberekera kumudzi, adzayenera kuthamangira ku chipatala pasanathe tsiku kuti akalandire chithandizo choyenera.

Page 10: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

10 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

Kumeneko awafotokozera zizindikiro zoopsa kwa mayi wobereka kumene monga izi:• Mutu kupweteka.• Kutuluka ukazi wochuluka.• Kuchita manjenje kapena kukomoka.• Kusanza kapena kutsekula m’mimba.• Kuphwanya m’thupi kapena kupweteka

msana.• Kutuluka magazi kapena fungo ku malo

obisika.• Kumva kupweteka kwambiri pa chifuwa

kapena kupuma movutikira.• Kutupa kwa miyendo kapena kufiira

mawere (mabere).• Kukodzedwa.• Kumva kupweteka kwambiri potaya

madzi.

Zinthu zomwe Mele ndi Joni ayenera kukumbukira ndi izi:• Kumufunditsa ndi kumuveka mwana

zovala zouma bwino komanso kuonetsetsa kuti nthawi zonse mutu wa mwana suli pa mphepo.

• Mele ayenela kulandira vitamini A akangobereka kapena pasanathe masabata asanu ndi anayi (8).

• Kuonetsesa kuti maso a mwana ndi aukhondo nthawi zonse.

• Kupita ku chipatala pakatha masiku asanu ndi awiri (7) akangobereka kuti iye ndi mwana wake akayezedwe ngati ali bwino ndi kulandira chithandizo choyenera.

• Kupita kukayezetsa kawirikawiri kuti adziwe ngati ali ndi kachirombo ka

KuberekaMele ndi Joni anakonzekera kukaberekera mwana wawo ku chipatala.

Kusamalira mwana wakhandaPofuna kupewa matenda omwe ali oopsa kwambiri kwa ana akhanda, mwana amafunika chisamaliro chachikulu miyezi yoyambilira ya moyo wake.

HIV. Iyi ndi njira yoyamba yothandiza kupewa kachirombo ka HIV kuchokera kwa mayi kupita kwa mwana.

• Kusankha njira yolelera mwachangu pamene mwana wabadwa.

• Kuganizira zochita mdulidwe wa mwana wawo yemwe ndi wamamuna.

Page 11: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

11 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

Kadyedwe ka mayi ndi mwana wakhanda

• Mele anayamba kuyamwitsa mwana mphindi makumi atatu (maminiti 30) zoyambilira kuchokera pa nthawi imene mwana anabadwa. Izi zinathandiza kuti mwana wake ayamwe mkaka wa chikasu woyambilira umene umateteza mwana ku matenda osiyanasiyana.

• Mele akaona kuti mkaka ukuchedwa kutuluka kapena ukuchepa, amamuikabe mwana kubere ndi kumulimbikitsa. Izi zimathandiza kuti mkaka uyambe kutuluka moyenera.

• Mele amayamwitsa mwana wake bere limodzi mpakana mkaka uthe. Kenaka amayamba kuyamwitsa bere lina mpakananso mkaka uthe. Izi zimathandiza kuti mwana wake ayamwe mkaka wokhathamira wapansi pa bere womwe umathandiza kuti mwana akule mwathanzi.

• Meleamayamwitsamwanawakemkakawam’maberewokhawokhakufikirapamenemwanawakeadzafikemiyeziisanundiumodzi(6).Izizimathandizamwanakupewamatenda otsekula m’mimba, achifuwa komanso achibayo.

• Monga mayi woyamwitsa, Mele amadya chakudya choonjezera kamodzi pa tsiku ndi kumwa zakumwa zosiyanasiyana zamadzimadzi. Izi zimathandiza kuti Mele akhale ndi thanzi komanso mphamvu zoyamwitsira mwana.

Page 12: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

12 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

Mele ndi Joni amasangalala akamaona mwana wawo akukula. Njira zina ndi izi zomwe amatsatira kuti mwana wawo akule bwino ndi thanzi:

• Kulandiritsa mwana wawo vitamini A pakatha miyezi isanu ndi umodzi (6) iliyonse.

• Kugwiritsa ntchito mchere wa Ayodini (Iodine).

• Kutsatira masiku akatemera mwandondomeko.

• Kulandiritsa mwana wawo mankhwala a njoka za m’mimba.

• Mele ndi Joni amaonetsetsa kuti iwo ndi mwana wawo agona mu neti yonyikidwa m’mankhwala opha udzudzu usiku uliwonse chaka chonse.

• Amapewa matenda otsekula m’mimba posamba m’manja ndi sopo:1. Asanayambe kuyamwitsa.2. Asanakonze chakudya.3. Asanadye.4. Akachokera ku chimbudzi.5. Akamusintha mwana thewera.

• Chakudya chosavindikira ndi chozizira chikhoza kutsekulitsa m’mimba. Nthawi zonse amavindikira chakudya chawo ngati sichikudyedwa.

• Amakonza chakudya cha mwana mu nthawi yomwe akufuna kumudyetsa.• Mele ndi Joni anakumba chimbudzi ndipo amachigwiritsa ntchito nthawi zonse.

Wa zaumoyo anafotokozera Mele ndi Joni kuti ngati aona zizindikiro izi, apite ku chipatala mwachangu:• Kupuma mobanika kapena mofulumira.• Kutentha thupi.• Chimbudzi cha madzimadzi katatu pa tsiku.• Kusanza kangapo pa tsiku.• Kugona mopitilira.• Kuchita manjenje kapena kukomoka.

Kusamalira mwana akamakula

Kuteteza mwana ndi banja ku matenda

Kudziwa zizindikiro zoopsa kwa mwana

Page 13: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga

13 Mfundo zothandiza banja la tsopano Kuti likhale lathanzi ndi losangalala

Maulendo asanu

5

Khalani ndi banja

losangalala komanso la

thanzi.

MANAMBALA A LAMYA (FONI) OFUNIKIRADzina Nambala ya lamya (foni)

Ana onse ayenera kulandira katemera kuti atetezedwe ku matenda osiyanasiyana. Ndikofunika kwambiri kuti katemera aliyense alandiridwe mu nthawi yake. Kuti atetezedwe, mwana wa Mele ndi Joni akuyenera kulandira katemera yense kuyambira sabata yoyamba mpaka mwezi wa chisanu ndi chinayi (9).

Katemerayu amateteza mwana ku matenda osiyanasiyana monga chifuwa chachikulu cha T.B, chikuku, kupuwala kwa ziwalo, matenda owumisa ziwalo ndi owumitsa khosi, chibayo, kutsekula m’mimba ndi matenda ena.

Katemera

Page 14: Zamkatimu - k4health.org ndi chisamaliro cha wina ndi mzake. Mele ndi Joni amakondana kwambiri ndipo amafuna atakwatirana. Pokonzekera moyo wawo wa m’banja amakambirana zinthu monga