CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M...

49
Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele Ambuye akudalitseni inu, m’bale. Mmawa wabwino, abwenzi. Kuli kotentha kwambiri, kuti tikhale mu kachisi mmawa uno, koma chaumelero kwambiri kukhala tiri muno. Wokondwa kwambiri kuti tikanakhoza—tikanakhoza kulowa muno lero chifukwa cha msonkhano uno. Ndipo ndadzipereka kuti ndikanakhala nako kuphunzira tsopano pa Masabata Makumi Asanu Ndi Awiri A Daniele awa. Zimenezo zikulumikizana nawo Uthenga wonse ine ndisanati ndipitirire nazo—Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri. Zomwe pali, Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri; Miliri Isanu ndi iwiri; Malipenga Asanu ndi awiri; Matsoka Atatu; mkazi mu dzuwa; kuponyedwa kwa Mdierekezi wofiira; wani handiredi forte foro sauzande akusindikizidwa; zonsezo zikuchitika pakati pa nthawi iyi. Ndipo ine ndinaganiza kuti ndinayenera nditengeremo kaye izi poyamba. 2 Tsopano, kuli kotentha. Ife sitiri kulinga kuti tikhale motalika kwambiri, basi momwe ife tingathere. Ndipo iyi ili nyengo, kawirikawiri, nyengo yopuma, imene pamene anthu samakhala ali ku mpingo mowirikiza kwambiri. Ndipo, makamaka, ndi ena onse a iwo ali nazo zipinda za mpweya wabwino, ndi zinazotero, momwe muli mwawofuwofu. Ife tikukhumba tikanati tikhale nazo izo, koma pa nthawi ino ife tiribe izo. 3 Ochuluka a makolo athu akale ankakhala panja mu dzuwa lotentha. Pamene ine ndilingalira za kupepesa kwa anthu chifukwa cha kusakhala ndi chipinda cha mpweya wabwino, malingaliro anga nthawizonse amabwerera mmbuyo ku Afrika kumene iwo anagona pansi mu mikuntho imeneyo, ndipo akazi amenewo ndi tsitsi lawo likugwera pansi mu nkhope yawo, ankagona pamenepo usana ndi usiku womwe, nkusachoka konse pa malo pamene iwo anali atagonapo; opanda kudya, kumwa, kapena kalikonse, kukhala apo pomwe kuti angomva Mawu, kapena awiri, apa ndi apo, a Ambuye. 4 Ine ndikukhoza kuganiza za Mexico pamene kuli kotentha kwambiri, moonamtima, ine ndinakhala mu chipinda cha mpweya wabwino ndi kumayesa kudzikupizira ndekha, iko kunali kotentha kwambiri. Ndipo kumawawona anthu amenewo akubwera kumeneko ili 9:00 koloko mmawa, mwamukulu mwa masewero umo, ndipo mopanda mpando, kuti ukhalepo pansi. Anthu odwala, odwala kwenikweni, oti afa, odwala; khansara, chotupa; ndi amayi odwala, aang’ono, ana oti afa ndi chirichonse, ataimirira apo pomwe mu dzuwa lotentha mowira, wopanda mthunzi paliponse, ndipo basi kungotsamirana wina ndi mzake kuchokera naini koloko mmawa mpaka naini usiku

Transcript of CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M...

Page 1: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele

Ambuye akudalitseni inu, m’bale. Mmawa wabwino,abwenzi. Kuli kotentha kwambiri, kuti tikhale mu

kachisi mmawa uno, koma chaumelero kwambiri kukhala tirimuno. Wokondwa kwambiri kuti tikanakhoza—tikanakhozakulowa muno lero chifukwa cha msonkhano uno. Ndipondadzipereka kuti ndikanakhala nako kuphunzira tsopano paMasabata Makumi Asanu Ndi Awiri A Daniele awa. Zimenezozikulumikizana nawo Uthenga wonse ine ndisanati ndipitirirenazo—Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri. Zomwe pali, ZisindikizoZisanu ndi ziwiri; Miliri Isanu ndi iwiri; Malipenga Asanundi awiri; Matsoka Atatu; mkazi mu dzuwa; kuponyedwakwa Mdierekezi wofiira; wani handiredi forte foro sauzandeakusindikizidwa; zonsezo zikuchitika pakati pa nthawi iyi.Ndipo ine ndinaganiza kuti ndinayenera nditengeremo kaye izipoyamba.2 Tsopano, kuli kotentha. Ife sitiri kulinga kuti tikhalemotalika kwambiri, basi momwe ife tingathere. Ndipo iyiili nyengo, kawirikawiri, nyengo yopuma, imene pameneanthu samakhala ali ku mpingo mowirikiza kwambiri. Ndipo,makamaka, ndi ena onse a iwo ali nazo zipinda za mpweyawabwino, ndi zinazotero, momwe muli mwawofuwofu. Ifetikukhumba tikanati tikhale nazo izo, koma pa nthawi ino ifetiribe izo.3 Ochuluka a makolo athu akale ankakhala panja mu dzuwalotentha. Pamene ine ndilingalira za kupepesa kwa anthuchifukwa cha kusakhala ndi chipinda cha mpweya wabwino,malingaliro anga nthawizonse amabwerera mmbuyo ku Afrikakumene iwo anagona pansi mu mikuntho imeneyo, ndipo akaziamenewo ndi tsitsi lawo likugwera pansi mu nkhope yawo,ankagona pamenepo usana ndi usiku womwe, nkusachoka konsepa malo pamene iwo anali atagonapo; opanda kudya, kumwa,kapena kalikonse, kukhala apo pomwe kuti angomva Mawu,kapena awiri, apa ndi apo, a Ambuye.4 Ine ndikukhoza kuganiza za Mexico pamene kuli kotenthakwambiri, moonamtima, ine ndinakhala mu chipinda champweya wabwino ndi kumayesa kudzikupizira ndekha, ikokunali kotentha kwambiri. Ndipo kumawawona anthu amenewoakubwera kumeneko ili 9:00 koloko mmawa, mwamukulumwa masewero umo, ndipo mopanda mpando, kuti ukhalepopansi. Anthu odwala, odwala kwenikweni, oti afa, odwala;khansara, chotupa; ndi amayi odwala, aang’ono, ana oti afa ndichirichonse, ataimirira apo pomwe mu dzuwa lotentha mowira,wopanda mthunzi paliponse, ndipo basi kungotsamirana winandi mzake kuchokera naini koloko mmawa mpaka naini usiku

Page 2: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

2 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

umenewo, kuti angomvetsera maminiti makumi atatu kupyoleramwa wotanthauzira, ndi kuwona ntchito za Ambuye. Atakhalapamenepo ndi kumayembekezera, atavala zovala zazikuluzolemera zachikale, iwo amavala izo mu dzinja ndi chirimwe.Ndizo zonse zomwe iwo ali nazo.5 Ndiyeno ine ndikuganiza za kugona kunja uko munkhalango zimenezo, momwe iwo amabweretsera umo anthuodwala amenewo, omwe samakhoza ngakhale kusuntha. Ndipomu India, pamene iwo amakhoza kuwunjikizana wina pansi,ndiye nkumugoneka mmodzi pamwamba pa mmodzi ameneyo,mmodzi pamwamba pa mmodzi uyo, monga choncho, ali ndikhate ndi matenda; kumene ankawakhwekhweleza iwo podutsa,ndi kuchokera mu misewu, ndi kuwaika iwo mu kutenthakumeneko, kowira, dzuwa la mzigawo zotentha. Mu mikuntho,ndi mphenzi zikung’anima, ndi zinthu monga zimenezo, iwoamakhoza kugona pamenepo pomwe mu dzuwa limenelo ndimkuntho, ndi chirichonse, ndipo opanda kusuntha konse kapenakudandaula, basi…ali kuyesa kuti amve Mawu a Mulungu, apandi apo, chinachake kwa moyo wawo. Ndiye nchifukwa chiyanikuti ife tizipepesa mmawa uno, tiri ndi denga pamwambapa mutu wathu, zokupizira zikuzungulira? Ife tiyenera kutitizichita manyazi ngati ife tikudandaula za izo.6 Kotero ine ndikukumbukira osati kale litali, mu chilumba,chimodzi cha zilumba kunja mu Nyanja za Kummwera, inendinali kuchititsa msonkhano kumeneko usiku umenewo.Ndipo, o, uko kunabwera mkuntho. O, ine sindinayambendawonapo mkuntho woterowo, kungokhala kung’animakumodzi kwa mphenzi pambuyo pa kumzake, kuliwalitsadzikolo. Ndipo momwe mphepo zimawombera mpakanamitengo inali lambilambi pansi. Ine ndinati, “Chabwino, iwoali…Ine ndikhoza kungovula suti yanga, chifukwa sikukakhalamunthu aliyense kumusi kumeneko.”7 Mu mphindi pang’ono galimoto yaying’ono inadzaima pachitseko, ndipo winawake anagogoda pa chitseko, okonzeka kutitizipita.

Ndipo ine ndinati kwamnyamata, iye amakhoza kuyankhulaChingerezi, ine ndinati, “Alipo aliyense kumusi kumeneko?”

Anati, “Inu simungakhoze nkomwe kupeza mtunda wamdadada wa mu mzinda ku malowo,” pa bwalo lalikulula mpira.

Ndipo ine ndinati, “Inu mukutanthauza kuti anthu ali—alikunja ukomonga choncho,” ine ndinati, “mkunthowonse uwu?”

Iwo anati, “Iwo akufuna kuti amve zaMulungu.”8 Ndipo—ndipo chotero ine ndinapita kumusi uko. Ndipokumeneko kunali madona, asungwana aang’ono, azakazongopitirira khumi, osati akufwentheza ndi kuseka, ndikumatutumitsa chingamu, ndi kumayankhula za bwenzi lawo.

Page 3: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 3

Mawu aliwonse, iwo amangogonekera kwa Iwo; ndipo osasunthakonse, anangokhala ndi kumamvetsera. Kupanga kuitanira kwaku guwa, kungopanga kuitanira kwa kuguwa chabe, ndipo zikwizinaimirira, ali ndi misonzi ikutsika kuchokera mmaso mwawomonga choncho, ali ndi manja awo mmwamba kwa Mulungu,akufuna chifundo kwa miyoyo yawo, asungwana aang’ono ndianyamata, ausinkhuwa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri, khumindi zisanu ndi zitatu. Tsopano ndi kovuta kuti uwafikitse anthuachikulire omwe ngakhale kuti amvetsere, inu mukuona. Izo—izo zikusonyeza kuti ife tiribe kanthu koti tizidandaula nako.Mayamiko akhale kwaMulungu! Inde, bwana.9 Ife tikufuna kuti tizikhala nazo zonse mwamakono mongaAmereka yense, koma ife tiribe izo mwanjira imeneyo; kotero ifetizingochita ndi zomwe ife tiri nazo.10 Tsopano, ine ndiri nako kanthu kakang’ono kamene inendinakazindikira kamene ine ndikanafuna kuti ndikachitemuno mu kachisi kachiwiri. Ndi angati ali nawo Mabaibulo,kwezani dzanja lanu. Zabwino. Tiyeni titembenuzire kuMasalmo 99 ife tisanati tikhale nalo pemphero. Ife tinkakondakuchita izi, M’bale Neville, zaka zapitazo. Ine sindikudziwangati…Kodi inumwawerenga kale Salmommawa uno? [M’baleNeville akuti, “Ayi.”—Mkonzi.] Ayi. Ine ndimangokonda kuti,osonkhana, kuti aziwerenga lina la Salmo.11 Mmawa uno, pamene ine ndinali nditakhala mu chipindachanga chowerengera, ndikusinkhasinkha pa Uthenga uwu ndiMawu, ine ndinaganiza, “Inu mukudziwa, icho chikanakhalachabwino kachiwiri kukakhala—kukakhala nawo iwo onse kutiawerenge Salmo. Ine ndimazikonda izomwabwino kwambiri.”

Chifukwa chimene ine ndinachedwera pang’onopo, ndinalindi kuitana kwa kutali, kuchokera ku Cheyenne, kotero ndichochifukwa ine ndinali.12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmoili, ine ndiri nazo zolengeza zina zoti zipangidwe, zomwezangopatsidwa kumene kwa ine. Ndilo Salmo 99.13 “Kuyambira lero, zolengeza zonse zokhudza misonkhanopano pa kachisi, ndi mu yokopa anthu, zizichokera kuofesi ku Jeffersonville. Aliyense wokhumba kuti adziwe zamisonkhano ayenera kulembetsa, kapena kupereka dzina lawondi adiresi, ndi kuziyika izo pa guwa pa kutseka kwamsonkhanousikuuno. Chidziwitso chizitumizidwa kwa inu mu nthawikuti inu muzipanga kukonzekera kuti mudzakhale nawo pamisonkhanoyo.”

Izo ziri, ngati munthu winawake mtsogolo akufuna kutiadziwe basi kumene ife titi tikakhale nayo misonkhano, ife tirinako kachitidwe komwe takhazikitsa, ku ofesi uko tsopano,koti inu mukhoze kungosiya dzina lanu ndi adiresi pano.Ndipo ife tidzakutumizirani inu khadi, nthawiyo isanakwane,

Page 4: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

4 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

kotero kuti muzidziwa komwemisonkhano ili kuchitikira, ndipomwinamwake mitu yake, ndi zina zowonjezera zomwe ziripo,ngati inu mungakhoze kupeza mwayi. Inu mukuona, ngati iweulibe malo ovomerezeka komwe izo zikuchokera, wina amanenaizi ndipo wina amanena izo, iwe—iwe sumazimva izo, inumukuona. Kotero mungolola…Lembani apo dzina lanu ndiadiresi ndipo muziike izo pano, ndipo Billy Paul azitenga izondipo azidzazipereka zimenezo.14 Tsopano, izo zinafunsidwa, panonso, ngati pakanatipakhale enanso… “M’bale Branham, kodi muzikhala nayomisonkhano inanso ya machiritso mu kachisi, ndi kuzindikiraza mmitima?” Ayi. Ayi. Kuzindikira za mmitima kuziperekedwandi—ndi gulu lathu lina. Ife tiri naye M’bale Neville panotsopano yemwe ali nayo mphatso ya ulosi, yemwe amaloserapa odwala ndi kuzindikiritsa kwa iwo zinthu zomwe iwoakuzisowa kuti azidziwe. Ndipo ife tiri naye m’bale dzina lakeHigg-…Higginbotham, mmodzi…anali trastii, anatumikiramokhulupirika pa gululo. Ine sindikumuwona iye mmawa uno,koma iye kawirikawiri amakhala nayo mphatso ya kuyankhulamu malirime. Ndi dona wamng’ono wotchedwa Arganbright,mlongo wamng’ono wokondedwa yemwe ali nayo mphatso yakutanthauzira malirime.15 Ndipo mauthenga awa akutsimikizira kuti ali a Mulungu,chifukwa iwo kwenikweni sali kumabwera kunja kwadongosolo, iwo akungoikidwamudongosolo. Ndipo posakhalitsapamene mphatso izi ziziyamba kuchulukana, ife tati tidzayeseku—kutenga…kufika pozikhazikitsa izo kumene mu mpingo,njira yochitira izo. Ndipo ine ndikuti ndiwawone iwoposachedwa ndithu, ndi chotero kuti—kuti—misonkhanoizidzakhala ikuchitidwa mwangwiro basi mu dongosolo laAmbuye,monga ife tingakhoze kuitengera iyomwangwiro.16 Koma anthu okondedwa awa, amatero woyandikananaye wanga, Akazi a Woods, omwe anali nayo maikorofoniatalumikiza kuno, ndi tepi kumbuyo uko, kuti ajambulemsonkhano, basi mwacholinga choti awajambule mauthengaamenewo, ndi kukawalemba iwo, ndi kuwona ngati iwoakulondola kapena ayi. Mwaona? Ndi momwe iwo akufufuziraizo. Ine ndikuwadziwa Akazi a Woods kuti ali mkaziwoonamtima.Ndipo iwo akundiuza ine za zinthu zambiri zomwezakhala zitanenedwa, zikufika pochitika.17 Tsopano, kotero ife tiri oyamikira chifukwa cha zimenezo.Ndi chitonthozo bwanji chimene chiri kwa ine kunyumba,pamene ine ndinabwera kunyumba, ndiye. Kuzindikira zammitima uko pa mbali ya uneneri kumangonding’ambira inepansi, ndipo, kotero, Mulunguwanditumizira ine chondipumitsachina pa zimenezo, kupyolera mu ulosi, ndi kuyankhula mumalirime, ndi kutanthauzira, zomwe ziri ulosi. Zomwe, ziri ulosi,kuyankhula mu malirime. Pali anthu awiri osiyana akulosera.

Page 5: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 5

Mmodzi akuyankhula, mmodzi winayo akumvetsa zomwewinayo akunena mu malirime osadziwika, ziri chimodzimodziulosi. Ndipo tsopano ife tidzakhala…Ife timakhala nazozimenezo tsiku lirilonse, msonkhano uliwonse kuno pamene ifetikhala ndimizere yathu ya pempheromumsonkhano.

18 Tsopano, apa pangakhale wina ndiye akanati afunse,kodi…za mphatso. Inde, ine ndikanali nayobe iyo. Komamwanjira imeneyo, njira yokha yomwe ine ndimaigwiritsiraiyo ntchito, ndi pa zoyankhulana mwapadera, zomweine ndimakhala nazo. Ndipo, kuti mukhale nazo izo, inendikukhulupirira iwo ali nazo izo pa bolodi la zolengezakumbuyo uko, kuti mupeze chilolezo ndi kuyiika nthawi yanumu dongosolo, ndi Billy Paul, mnyamata wanga, ya kuno kapenamu misonkhano ukatha uno. Kunja mminda, kulikonse, inumuyenera kukhala nalo khadi laling’ono lomwe Billy Paulati akupatseni inu. Ngati pali chinachake mu moyo chimeneinu simungakhoze kuchimvetsa, ndipo simukudziwa momwemungatulukire mu icho, ndipo inu mukufunafuna nzeru yaAmbuye, ndiye lolani…Muoneni Billy Paul, mwana wanga,yemwe ali mlembi, ndipo iye akupatsani inu khadi laling’ono,ndi kukuikirani inu tsiku, pa nthawi yake.

Ndiyeno pamene ife tikukhala nazo zoyankhulana zimenezo,ndiye apo pazikhala pamene ife tizipita mkati limodzi, inunokha ndi ine. Ndipo ngati ali akazi akubwera, inu muzipitamkatimo nane ndi mkazi wanga. Ndiyeno inu… Ife tizifufuza,ndi kufunafuna Ambuye ndi kumupempha Iye chimene inumuyera kuchita.

19 Tsopano, zina, zovuta zazing’ono ndi zina zotero mongazimenezo, zaperekedwa kwa M’bale Neville, ndi M’baleHigginbotham, ndi Mlongo Arganbright, ndi ena omweamayankhula ndi malirime ndi kutanthauzira, omwe ali panomu mpingo.

20 Chotero, ife tikuchita ngati ulendo. Ine ndikukhulupiriraanali Yetero yemwe ananena kwa Mose tsiku lina, onani,“Tiyeni titenge akuluakulu ena.” “Ndipo Mzimu wa Mulunguunatengedwa kuchokera kwa Mose ndi kuikidwa pa akuluakulumakumi asanu ndi awiri, ndipo iwo ankalosera. Komazinthu zazikulu ndi zovuta zokha zinkabwera kwa Moseyekha.” Tsopano, ife sindife Mose, ngakhalenso kuti awaali akuluakuluwo, koma ife tikadali kutumikirabe YehovaMulungu, tiri nalo Lawi la Moto lomwelo likutitsogolera ifeku Dziko lolonjezedwa.

Kotero, ndiye, inde, padzakhala pali ena, pazikhalamisonkhano ndipo pazikhala otanthau-…Kuzindikira zammitima kuzibwera. Zimenezo zizindipatsa ine mwayi ndiyekuti ndizikhala mu pemphero ndi kuwerenga, masiku amene

Page 6: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

6 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

ine ndikudziwa kuti zoyankhulana izi zikubwera, ndi kukhalawokonzekera izo.21 Tsopano kumbukirani, Billy Paul Branham, mlembi wathuwaku ntchitoyi, adza…Izo ziri…Zolengeza ziri pa bolodikumbuyo uko, ndi matrastii. Ine ndiri nacho cholembedwa panochoti ndilengeze zimenezo, ndi kuwauza anthu kuti iwo akhozakuwerenga izo pa bolodi la zolengeza, potuluka kunja.22 Tsopano, tsopano, mmawa uno ife tiri nalo phunzirolalikulu, ndipo usikuuno ife tidzayesa kuti tipitirize izo. Ndipo,ngati Ambuye alola, Lamlungu lotsatira, wina, mu izo. Inesindimadziwamomwe izo zinali kufikira mwakuyampakana inenditayamba kuziwerenga izo. Ndipo chikadali chinsinsi kwa ine,panobe, ndipo chotero ine ndikungodalira pa Ambuye.23 Tsopano, inu ndi Mabaibulo anu, tiyeni titembenuzireku Masalmo 99, 99. Ndipo ine ndiwerenga ndime yoyamba,osonkhana aziwerenga ndime ya 2, ndiye tonse palimodzitiwerenga ndime yotsiriza. Ife tipitiriza choncho; ine, ya 1;osonkhana, ya 2; ine, ya 3; osonkhana, ya 4; mpaka ku ndimeyotsiriza, ndiyeno ife tonse tiiwerenge iyo palimodzi.

Ife tingaime pamene ife tikuwerenga Mawu a Mulungu.[M’bale Branham ndi osonkhana akuwerenga Salmo 99:1-9monga iye wasonyezera—Mkonzi.]

YEHOVA akulamulira; siyani anthu anjenjemere: iyeakukhala pakati pa akerubi; siyani dziko lisunthidwe.

YEHOVA ndiye wamkuru mu Zioni; ndipo iye ali patalipamwamba pa anthu onse.

Asiyeni iwo alemekezeke dzina lanu lalikuru ndilowopsya; pakuti ilo liri loyera.

Mphamvu ya mfumu nayonso imakonda chiweruzo;inu mukhazikitsa zolunjika, inu mumachita chiweruzondi chilungamo mu Yakobo.

Mkwezeni inu YEHOVA Mulungu wathu, ndipopembedzani pa chopondera mapazi chake; pakuti iyeali woyera.

Mose ndi Aroni pakati pa ansembe ake, ndi Samuelimwa iwo akuitanira pa dzina lake; iwo anaitanira paYEHOVA, ndipo iye anawayankha iwo.

Iye anayankhula kwa iwo mu mtambo njo: iwoanasunga maumboni ake, ndi malangizo omwe iyeanawapatsa iwo.

Inu munawayankha iwo, O YEHOVA Mulungu wathu:inu munali Mulungu yemwe munawakhululukira iwo,ngakhale inu munabwezera kuwukira kwawo.

Page 7: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 7

Mkwezeni Yehova Mulungu wathu, ndipo pembedzanimu phiri lake loyera; pakuti Yehova Mulungu wathu aliwoyera.

24 Tiyeni ife tiweramitse mitu yathu.Zoonadi, Ambuye, Mawu awa analembedwa ndi kudindidwa

ndi wantchito Wanu, Davide, mu Salmo kwa Inu. Inumumakhala pakati pa Akerubi. Inu ndinu woyera, ndipophiri Lanu liri loyera. Tiloleni ife tiyandikire pafupi ndimitima yathu yokonkhedwa ndi Magazi a Ambuye Yesu, ndichikumbumtima changwiro, ndi chikhulupiriro ndi chitsimikizokuti ife tikubwera mu Kukhalapo kwa Mulungu wathu. Muloleomvetsera onse awa mmawa uno akhale molemekeza. Tsegulanimakutu athu a kumvetsa. Yankhulani kupyolera mwa ife, munzeru, kuti ife tikhoze kumadziwa momwe khalidwe lathuliyenera kumakhalira mu masiku ano ndi mu KukhalapoKwanu.25 Ife tikanati tikupempheni Inu, Mulungu wathu, kutimuwulule kwa ife zinthu za chinsinsi izi zomwe zakhalazitabisidwa zaka zonse izi, pamene ife tiri kuyandikirachimodzi cha chodzipereka kwambiri, Mawu otontholetsa.Inu munayankhula za izo pamene Inu munali pano pa dzikolapansi, ndipo munati, “Iye amene awerenga, msiyeni iyeamvetse.” Kotero, ife mwachisomo kwambiri tikubwera kwaInu, Ambuye, ndipo tikufunafuna nzeru Yanu, posadziwa basichoti nkunena. Ndaika mu dongosolo pano Malemba angapo,ndipo mwakachetechete ndi mwathunthu ndikudalira pa Inukuti mutipatsa yankho, pakuti palibe cholinga china komakuti ife tikhoze kudziwa ora limene ife tiri kukhalamo, kuti ifetikhoze kukhala okonzekera kwa zinthu zazikulu zomwe zagonamtsogolo. Kodi Inu simupereka izo kwa ife, Ambuye, mu Dzinala Iye Yemwe anatiphunzitsa ife tonse kuti tizipemphera mongachonchi! [M’bale Branham ndi osonkhana akupemphera limodzimolingana ndi Mateyu 6:9-13.—Mkonzi.]

…Atate athu omwe muli kumwamba, dzina lanuLilemekezedwe.Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe pansi

pano, monga izo ziri kumwamba.Tipatseni ife lero chakudya chathu cha patsiku.Ndipo mutikhululukire ife za kulakwitsa zathu,

monga ife tiwakhululukira iwo amene atilakwira ife.Ndipo musatitsogolere ife kukalowa mu mayesero,

koma mutipulumutse ife ku choyipa: Pakuti wanu uliufumu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, kwanthawizonse.Ameni.

26 Mukhoza kukhala pansi. Tsopano, ngati aliyense wa amunaakufuna kuti avule majekete awo, ingomvererani kulandiridwa.

Page 8: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

8 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

Ndipo iwo amene ali kuimirira mozungulira—mmbali ku khoma,ngati mapazi anu apweteka, bwanji, ingomvererani pa ufulukutuluka panja.27 Ndipo tsopano, ine ndikuganiza, ngati ana akufuna kutiapite ku zipinda zawo, kapena kodi iwo akhala atabalalitsidwakale? [M’bale Neville akuti, “Ayi, iwo sangakhoze. Ifesitingakhoze kukhala nayo iyo mmawa uno, pa chifukwa chaunyinji.”—Mkonzi.] M’busa akuti unyinji wapangitsa zipindakukhala zodzaza, kotero ife sitingakhoze kukhala nayo Sandesukulu ya aang’onowa. Ndipo ife tikadakhala okondwa ngati inuana aang’ono tsopano mukanati mugwirizane nafe ife, pamenemmawa uno ife tikukhala nawo, tikuyamba Uthenga wawukulu,wopambana umene ine ndikutsimikiza kuti utanthauza kuchitakwakukuru kwa abambo anu ndi amayi, ndi okondedwa anuomwe ali pano, ndipo ngakhale kwa inu aang’ono inu. Chotero,ife tiri kuyandikira izi molemekeza kwambiri.28 Ngati Ambuye akulola, mmawa uno ife tikutenga phunzirola masabata makumi asanu ndi awiri a Daniele. Ndipommawa uno ife tiyankhula pa Daniele ali mu ukapolo, ndipoGabrieli kuwulukira kumeneko kuti akamulangize iye zamtsogolo. PameneDaniele analimu pemphero, Gabrieli,Mngelo,anabwera mmenemo kuti adzamulangize iye.

Usikuuno, ine ndikufuna kuti ndiyankhule pa cholingachofutukuka pasanu ndi kamodzi cha kudzacheza Kwake,maphunziro asanu ndi limodzi osiyana oti abweretsedweusikuuno, chimene Gabrieli anadzera kuchokera.29 Lamlungu lotsatira, Ambuye akalola, ine ndikufuna kutindidzayike chifukwa ndi nthawi ya Mibadwo ya Mpingo Isanundi iwiri, ndi nthawi yomwe iyo ili, ndi pamene ife tirikuima lero. Zimenezo ndi Lamlungu lotsatira mmawa, Ambuyeakalola.30 Tsopano, chifukwa cha izi. Ine ndinabweretsa kuno zolembazina pang’ono kuchokera ku Mauthenga anga angapo otsiriza.Ndipo mmawa uno ine ndikufuna kuti ndilumikize apo,chifukwa izi ziri pa tepi ya maginito yomwe iti ipite konsekonsemdziko, mafuko ochuluka. Ndipo, nthawizonse, chifukwachimene ine ndimalumikizira za mmbuyo, ndicho mwinamwakewinawake akanadzamvera tepi kwa nthawi yawo yoyamba,ndipo sakanati akhale okhoza kumvetsa chimene ine ndinalikutanthauza pamene ine ndimalozera mmbuyo ku chinthuchinachake.31 Ife takhala tsopano kwa miyezi mu kuphunzira kwaBukhu la Chivumbulutso, Chivumbulutso Cha Yesu Khristu. Ifetabwera kupyola mu mibadwo ya mpingo. Mitu itatu yoyambaya Chivumbulutso inali mibadwo ya mpingo. Ndiye Yohaneanatengedwera mmwamba mu mutu wa 4 ndi wa 5, ndipoanawonetsedwa zinthu zomwe—zomwe zinali zoti zidzakhalepo

Page 9: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 9

zikadzatha izi kuno. Tsopano, pamutuwa 6, iye akutsikira pansimu dziko lapansi kachiwiri, kuti awone zinthu ziri kuchitikazomwe ziti zidzapite kuchokera pa mutu wa 6, ndime ya 1,mpaka mutu wa 19 ndi ndime ya 21. Mkati umu mukubweraZisindikizo, Miliri, Matsoka, dzombe, m—mkazi ali mu dzuwa,ndi kuponyedwa kunja kwa chinjoka chofiira, kusindikizidwakwawani handiredi forte foro sauzande, ndi zinthu zonse izi.

32 Ili lakhala liri sabata la kuphunzira kopambana. Dzulo,tsiku lonse, ine ndimalephera nkusuntha komwe kuchokeramu chipinda, kuyesera kuti ndiphunzire. Ndipo ndi chinachakemu nthawi yotsiriza, ambiri a anthu akale pano, zimene inendinkaphunzitsa, ine ndinkangoti, “Mkati umu muli masabatamakumi asanu ndi awiri a Daniele,” koma ine sindinali kuyeserakuti ndizikhudze izo, kuti ndizifotokoze izo. Koma nthawi ino,mwa chisomo cha Mulungu, ine ndadzitengera pa inemwinikuti ndiyesere kuti ndipemphe chisomo pamaso pa Mulungu,kuti ine ndikhoze kuzibweretsa izo kwa anthu. Ndipo mkatiumu ine ndikupeza zinthu zomwe ine sindiri kuzidziwa chinthuchimodzi chake.

33 Ndipo, ndiye, ine—ine ndakhala ndikuwerenga bukhu la Dr.Larkin, bukhu la Dr. Smith, zolemba za Dr. Scofield, ndemangazosiyana zochokera kwa amuna kulikonse, ndipo komabe inesindikukhoza kuika zawozo palimodzi kuti ndizipange izokutuluka apa bwino bwino. Mwaona? Kotero, sabata lino inendikukonzekera za, ndakhala ndikuchezera kobwereka mabukumu Kentucky, pa zina za akasidi zamakezana za makalendalandi nthawi, ndi kuzitenga izo kuchokera kobwereka mabuku,ndi zina zotero, mabuku onse achikale amene ine ndingakhoze,ndi pang’ono paliponse pamene ine ndingakhoze kuchita, ndikukhala nako kudalira kwanga mwakachetechete mwa YesuKhristu kuti awululire izo kwa ine.

Chifukwa, ine sindiri kufuna izo kuti ndizinena kuti,“Ine ndikuzidziwa izi, ndipo ine ndikuzidziwa izo.” Iyeakudziwa mtima wanga. Iye akumvetsera pa ine. Koma inendikufuna izo, kuti ine ndizikhoza kuwaunikira anthu Ake,chotero ine ndikukhulupirira kuti Iye azipereka izo kwa ine.Ine sindiri kuzidziwa izo panobe, koma ine ndiri kudaliraIye kwa Lamlungu likudzali, chifukwa ilo lidzakhala gawolopambana, Lamlungu likudzali, tidziwe ndi kukhazikitsamasabata makumi asanu ndi awiri amenewo.

34 Limodzi lirilonse liri nalo malo osiyana. Ndipo pamene iweutero, iwe umayenera kuti uwayendetse iwo onse modutsitsa,iwo samatulukira uko bwino, iwo samamveka bwino pamenepo.Izo sizingakhoze. Ndipo, chotero, ine—ine mwina sindikhozakukhala nazo izo molondola, koma ine ndikuti ndiwadalireAmbuye pa izo.

Page 10: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

10 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

35 Ndipo ine ndikukumbukira za Solomoni nthawi inaakupemphera ndi kuwapempha Ambuye Mulungu ngati Iyeakanati amupatse iye nzeru, osati za iyeyekha, “osati kutalikitsakwa masiku, osati moyo wautaliko, osati chuma,” komakuti iye akhoze kukhala nayo nzeru kuti azidziwa momwea—a—angamaweruzire anthu a Mulungu. Ndipo Mulunguanalemekeza pemphero limenelo, ndipo anamupatsa Solomoninzeru zimenezo, chifukwa izo zinali za kwa anthu Ake.Ndipo ndicho chifukwa ine ndikumupempha Mulungu kutiandirole ine ndidziwe chomwe makumi asanu ndi awiri awaa masabata akutanthauza, chifukwa ine ndikudziwa kutindiwo kalendara yolondola ya m’badwo umene ife tikukhalamouwu. Ndipo, chotero, ine ndikufuna kuti ndidziwe izo; osatikwa inemwini, ndine…osati kwa inemwini. Ndithudi, inendikufuna kuzidziwa izo. Ine sindikunena izo mwanjiraimeneyo, “Osati kwa inemwini,” chifukwa ine ndikuzifuna izokwa inendekha. Ine ndikufuna kuti ndidziwe, chifukwa inendikufuna kuti ndidziwe pamene ife tiri kukhala ndi nthawiyanji imene ife tiri kukhalamo. Ndipo, ndiye, ine ndikudziwakuti izo zinaperekedwa.36 Ndipo osiyana alingalira pa izo, ndipo iwo anali nazo izo kalemmbuyomo. Munthu mmodzi, ine ndinali kuwerenga, anali nazoizo zonse zikuthera mu 1919, za masabata makumi asanu ndiawirizi. Chabwino, izo sizinali chomwecho.

Kotero, atatha makumi asanu ndi awiri a masabata, atathamasabata makumi asanu ndi awiri, izo zonse zatha. Koteroife—ife sitiri…Ife tikufuna kuti tidziwe Choonadi. Ndipo inendikumupemphaMulungu kuti andipatse ine Choonadi.37 Tsopano, polinga kuti tiyikire kumbuyo izi, tipite mmbuyo,ine ndikufuna kuti ndibwereze pang’ono pokha za mmbuyo.Choncho, chotero, zolemba zina zimene ine ndinazilemba apa,zimene ife tinali nazo mu wa 5, mutu wa 4 ndi wa 5, koterokuti anthu akhoze kumvetsa. Poyamba, ife tisanachite izi, inendikufuna kuti ndizilumikize izo, kotero kuti inu mukhozekumva kuchokera pa wa 4…

Tsopano, kumbukirani, mutu wa 3 unali M’badwo waMpingo wa Laodikaya, ndipo Mpingowo unatengedwerammwamba pa kutha kwa Laodikaya.38 Tsopano, ine ndinali kuyesa kuti ndifotokoze chinachakekwa mkazi wanga za izi. Ine ndinali naye Becky, mwana wangawamkazi, ndi mitundu yonse yosiyana ya madikishonale ndizinthu zimene ife tikanakhoza kuzipeza. Iwo sali kuperekayankho. Ine ndiri nalo dikishonare la Baibulo. Ine ndirinalo dikishonare lakale la Chigriki. Ine—ine ndiri nalo—laWebsters ndi ena ambiri, madikishonare amakono. Palibe aiwo amakhoza kutenga ngakhale… kupereka mawu kapenamayankho, mwanjira iliyonse.

Page 11: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 11

39 Mkazi wanga anati, “Inu mungayembekeze bwanji anthuathu, omwe ali anthu osawuka, ndipo ambiri a iwo osaphunziramonga ife tiri, kuti amvetse zotero monga izo?”

Ine ndinati, “Mulungu adzapereka yankho.”40 Ziribe kanthu momwe ziriri zosokonezeka, Mulungu akhozakuzisungunula izo ndi kuzipanga izo mophweka. Pakutiife tiri…kagawo ka anthu amenewo omwe akukhumba,kupempherera tsiku limenelo ndi ora limenelo. Ndipo maso athualunjikidwa cha Kumwamba, ndipo ife tikuyembekezera KudzaKwake. Ndipo ine ndiri wotsimikiza basi kuti Iye atisonyezaife. Tsopano, iwo satiuza ife tsiku kapena ora, chifukwa palibemunthu akudziwa zimenezo, koma iwo ndithudi atiwuza ifetsiku la sabata limene ife tikukhalamo, ngati ife tingakhozekulipeza kokha ilo.41 Tsopano, mu mutu wa 4, Yohane anatengedwera mmwambamwamsanga, utatha Mpingo. Yohane, popita mmwamba, iyeanawona m’badwo wathunthu wa Mpingo. Apo ndi pameneine ndikukhumba kuti ndiyimepo, mphindi chabe, kutindinene, kuti: anthu ambiri amene ali kuyembekezera chinthuchachikulu, chopambana, champhamvu chinachake kutichichitike, mu m’badwo wa Amitundu, akulakwitsa ndithudi.M’badwo wa mpingo, ndi zonse izo zomwe ziti zidzachitike munthawi ya ulamuliro wa Amitundu, zalembedwa kuchokera paChivumbulutso 1 mpaka Chivumbulutso 3, kuphatikiza. NdiyeMpingo uli kukwatulidwa ndi kutengedwera mmwamba, ndipozina zonse za izi, mpaka ku mutu wa 19, ziri zimene zikuchitikakwa mtundu wa Ayuda, Mpingo utapita kale mmwamba. Ndipoiyo ndiyo nthawi ya Chisautso chachikulu, palibe chinthuchimene chikuchitika pakati pa Amitundu; kuphana kokha, ndizina zotero, monga ife titi tifike ku zimenezo ndi kuziwona.42 Koma Mpingo, Iwowokha, wapita pa wa 13…Pa ndimeyotsiriza ya mutu wa 3 wa Chivumbulutso, pamene M’badwo waMpingowaLaodikaya ukuthera, umene unali wotsiriza.43 Ndipo ife tinatenga m’badwo wa mpingo uliwonse, nthawiiliyonse, chinthu chirichonse chimene chinachitika, nyenyeziiliyonse, mtumiki aliyense, chikhalidwe chawo, zomwe iwoanachita, ndipo tinazibweretsa izo pansi pomwe kupyolera mumbiriyakale mpaka umodzi wotsiriza womwe, tinazijambulaapo pomwe pa chithunzi, pambali ya khoma. Ndipo pameneife tinali titatsiriza, Mzimu Woyera unabwera mkati ndipounadzapanga mkombero wa chinthu chomwe chinali pa khoma,ndipo unawulula izomwaWokha apa pomwe kwa ife tonse.44 Tsopano, mu kuchita izi, ine ndikudalira, pa kutha kwa iziIye adzabwera ndi chinachake chopambana ndi kutisonyeza ifekachiwiri kuti ife tiri pa mapeto a nthawi.45 Ndi angati a inu munamumva Kennedy…Zoyankhula zaPurezidenti Kennedy, ndemanga ndi zina zotero? Ndi angati

Page 12: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

12 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

amene anamva kuneneratu uku, kuti pofika Januwale 1,zanenedweratu kuti onse United States ndi Russia adzakhalaphulusa la chiphala cha moto? Ndizo zonse zimene ifetikuzisowa. Ndi mochedwa kuposa momwe ife tikuganizira.Mwaona? Kotero, ngati ife tiri pafupi chotero mpaka ngakhaleamuna a dziko lapansi lino akuneneratu chinthu chopambanaichi kuti chichitika, kulibwino ife tikhale pa tcheru, chirichonsechikhale chokonzedwampaka lero, kulapa konse kutapangidwa,chirichonse chitakonzeka, chifukwa ife sitikudziwa kungotinthawi yanji Ambuye wathu ati atiyitane ife. Ndipo pameneIye ayamba kuyitana, “Bwerani mmwamba muno,” ndibwinokuti tikhale okonzeka. Ndipo izo zidzabwera mu ora limene inusimuli kuliganizira.46 Chitsitsimutso chachikulu cha Chipentekoste tsopanochiri kutha. Ife tikuwona izo paliponse, kusuntha kwakukurukotsiriza. Uthenga wapita konsekonse. Chirichonse chirichokonzeka tsopano, kuyembekezera. Mpingo wasindikizidwauzipita. Oipa akuchita zoipa mochuluka. Mipingo ikukhala mwampingo kochuluka. Oyera akubweramoyandikira kwaMulungu.Mphatso za Mzimu zikuyamba kuchulukana mu timagulutating’ono. Ife tiri pa nthawi yotsiriza. O, ine ndimaikondanyimbo ija yomwe ife tinkakonda kuimbamumpingo.

Ine ndikuyembekezera kudza kwa Tsikulokondwa la zaka chikwi lija,

Pamene Ambuye wathu wodala atiadzabwere ndi kudzatenga Mkwatibwi Wakewoyembekezera apite;

O, mtima wanga uli kulira, kuchita ludzuchifukwa cha tsiku limenelo la kumasukakokoma,

Pamene Mpulumutsi wathu ati adzabwerereku dziko lapansi kachiwiri.

47 Kuyembekezera ora limenelo! Tsopano, mu mutu wa 5 ndindime ya 5, ife tikupeza, mu phunziro lathu lapitalo, kutiife tinayankhula za Wowombola Wachibale uja, yemwe ifetinapeza kuti anali Khristu. Tinazifanizitsa izo ndi Rute: Rutekulingalira; Rute kutumikira; Rute kupumula. Kulingalira,kunali kulungamitsidwa; kutumikira, kudzipanga yekhakukonzekera, kuyeretsedwa; kupumula, anali nawo MzimuWoyera, mpaka Mgonero wa Chikwati utadza. Ndi zokongolabwanji!48 Mpingo unabwera kupyolera mwa Joni Wesile,kulungamitsidwa, kapena…Marteni Lutera, kulungamitsidwa;kupyolera mwa Joni Wesile, kuyeretsedwa; kupyolera mwaAchipentekoste, ubatizo wa Mzimu Woyera; ndipo tsopano,kupumula, kuyembekezera Kudza kwa Ambuye Wake.Mwangwiro!

Page 13: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 13

49 Wotiwombola wathu Wapachibale, akuluakulu analikulondola pamene iwo anamutcha Iye Mwanawankhosa,alipafupi kuti akhale Mkango, monga woweruza. Iyeanali Mwanawankhosa, inu mukudziwa, ali nalo Bukhulosindikizidwa-kasanu ndi kawiri. Pamene Bukhulolinatengedwa, ntchito ya ukhalapakati inali itatha.50 Tsopano, mu mutu wa 3, Mpingo unali utapita mmwamba,koma tsopano chiwombolo chiri choti chiwululidwe, momweMpingo unawombo—unawomboledwera, vumbulutso la zomwezinachitika mu nthawi ya m’badwo wa Mpingo. Onani, Mpingowapita, kotero Iye ali tsopano kusonyeza, mu mutu wa 5,momwe Iye anachitira izo, zomwe zinachitika, momwe Iyeanawusindikizira Mpingo natsiriza. Vumbulutso la DzinaLake; ubatizo wa madzi, kugwiritsa ntchito Dzina Lake;Moyo Wamuyaya; kulibe gehena Yamuyaya; mbewu yaserpenti; chitetezero Chamuyaya; ziphunzitso zazikulu zonse,kukonzedweratu, kwa Mpingo, zomwe zinawululidwa kwaMpingo. Iye akusonyezamomwe Iye anachitira izo.51 Tsopano, Wapachibale wathu watenga Bukhulosindikizidwa-kasanu ndi kawiri la Chiwombolo kuchokerakwa Mwiniwake wapachiyambi. Ameni! Anali ndani, yemweife tinamupeza anali Mwiniwake wapachiyambi? MulunguMwiniwake. “Ndipo Mwanawankhosa anabwera ndipoanadzatenga Bukhu kuchokera ku dzanja lamanja la Iyeyemwe anakhala pa Mpandowachifumu.” Mwanawankhosaanali ndani? Wowombola, Wotiwombola wathu Wapachibale,Wapachibale kwa Mpingo, Yemwe anabwera ndipoanadzawombola Israeli.52 Tsopano ife tifika polowa mu zimenezo mmawa uno.Israeli anawomboledwa, koma izo sizinagwiritsidwe ntchitokwa iwo, chifukwa iwo anamukana Iye. Koma, Mpingounalandira chiwombolo chawo, ndipo Iye ali WotiwombolaWathu Wapachibale. Monga Boazi anachita kumuwombolaNaomi, polinga kuti amutenge Rute, wa Chimoabu, mlendo,Waamitundu; chomwechonso Khristu anawombola Israeli,anagwiritsa ntchito chiwombolo, ndipo anakanidwa.53 Inu mukukumbukira chikhululukiro, cha munthu yemweanawomberedwa, chimene ine nthawizina ndimachinena? Munthawi ya nkhondo ya pachiweni, pamene…Iye anali munthuwabwino. Iye anali wosalakwa, ndipo iwo anamupeza iyewolakwa. Ngakhale, iye anali wolakwa mwanjira, yakutiiye anathawira kwina mu nthawi ya nkhondo. Ndipo iwoanamupeza iye wolakwa ndipo anali oti akamuwombere iye.Ndipo munthu anapita kwa Purezidenti Lincoln ndipo anati,“Bambo Lincoln, uyu ndi munthu wa Chikhristu. Iye analikuwopa. Mnyamatayu, ine ndikuwadziwa makolo ake. Iye analikungochita mantha. Iye sanali kutanthauza choipa chirichonse.Iye anathawira kwina.” Anati, “Bambo Lincoln, izo ziri

Page 14: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

14 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

mmanja mwanu. Ndinu mmodzi yekha yemwe mungakhozekumukhululukira iye.”

Bambo Lincoln anatenga kachidutswa ka pepala ndicholembera chake, ndipo analemba, “Wakhululukidwa,”Wakuti-ndi-wakuti uyu. “AbrahamLincoln.”

Iye anathamanga kubwerera ku ndende, ndipo iye anati,“Ndi ichi pano. Ine ndapeza chikhululukiro chako.”54 Ndipo munthuyo anati, “Ine ndikukana kuti ndiyang’anepa icho. Icho chikanakhala chiri nacho chisindikizo chachikulupa icho. Icho chikanakhala chiri chirichonse. Iwe ukungoyesakuti undipange ine chinthu chosekedwa. Uyu si AbrahamLincoln. Munthu aliyense akanakhoza kulemba dzina lakelo.Koma icho chikanakhala chiri chovomerezeka ndi chisindikizochake, ndi zina zotero, ngati icho chikanati chichokere kwa iye.”Ndipo munthuyo anamukakamiza iye; ngakhale munthuyo analimu ndende anali kuganiza kuti uyo anali kuserewula, ndipoanangochoka napita.

Mmawa wotsatira, iye anawomberedwa. Ndiyeno iyeatawomberedwa kale, ndiye panali mulandu wa mu bwalolamilandu la feduro, chifukwaAbrahamLincoln,maoramakumiawiri ndi anai munthuyo asanawomberedwe, analemba dzinalake kuti munthu uyu anali atakhululukidwa. Ndiyeno bomalinamuwombera iye, chonchobe. Ndiye chiyani? Ndiye bwalolamilandu la feduro la United States, linati, atafika pa lingaliroili la bwalo lamilandu la Feduro, anati, “Chikhululukirosichiri chikhululukiro kupatula icho chitalandiridwa ngatichikhululukiro.”55 Ndipo Yesu anamuwombola Israeli pa Kalvare. Koma ichosichinali chikhululukiro kwa iwo, chifukwa iwo sanachilandireicho ngati chikhululukiro. Koma, mu phunziro lathu tsopanopa masabata makumi asanu ndi awiri awa, ife tipeza kuti iwoakubwerera ndi kudzalandira chikhululukiro chawo. Koma, Iyeanawuombola Mpingo, ndiye ife takhululukidwa chifukwa ifetalandiraMagazi a YesuKhristu ngati chikhululukiro chathu.56 Tsopano, ife tikupeza kuti Iye anali Wotiwombola wathuWapachibale, ndipo Iye anatenga Bukhu kuchokera mu dzanjala Mwini wapachiyambi. Ilo ndilo chikalata chaumwini kwachiwombolo. Ife tinapeza izo. Inu mukukumbukira kuphunzirakuja? Ilo ndi chikalata chaumwini cha chiwombolo. Ilo ndichikalata chovomerezeka kukhala nacho, kuti Mulungu anafunamoyo kwa imfa, mmunda wa Edeni. Ndiye, Yesu, Mmodziwolungama, anafa ndipo anatenga chikalata chaumwini, ndipoanali wokhoza kumatula Zisindikizo, kuwulula zomwe zinalimkati Mwawo; ndi kupereka cholowa, chimene chinali cha Iye,kwa anthu Ake. Moyo Wamuyaya, umene Iye anawulandira pakuchita izo, Iye anapereka Moyo Wake Womwe kumbuyo uko,paKalvare, ndipo anawugawaniza iwo pakati pathumwaMzimu

Page 15: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 15

Woyera. Ameni! Palibe munthu (sanati) ayambe wakhoza kufikapoti aganize ngakhale chikondi chimene icho chinali, chimeneIye anachita!

57 Satana, yemwe anayamba wakhala nacho chifukwa chakugwa mmunda akumangidwa ndi kuponyedwa mu Nyanja yaMoto. Masiku ake atha.

58 Yesu, mu Uthenga, anali nawo maudindo anai.Ife tinazigwira izo. Mwana wa Davide, wolowa kuMpandowachifumu; Mwana wa Abrahamu, ufumu wopatsidwa;Mwana wa munthu, wolandira dziko lapansi; Mwana waMulungu, wolandira zinthu zonse. Ufumuwopatsidwa!

59 Mu Chipangano Chakale, chuma sichinali kukhozakukhala—sichinali kukhoza kukhala chitatengedwa motalikakuposa zaka makumi asanu. Icho sichinali kukhoza kukhalachothetsedwa kuchokera kwa mwiniwake wapachiyambikupatula zakamakumi asanu.Ndipo pa tsiku lamakumi anai Iyeankalipira mtengowo. Pa tsiku la makumi asanu, chiwombolondi mphamvu zomwe zinali za Mpingo, zimene zinali zitatayikammunda wa Edeni, zinawomboledwa mobwerera, ndipozinatumizidwa kwa ife mwa ubatizo wa Mzimu Woyera, patsiku la makumi asanu.

60 Ndiye ife tinatenga izi, mpukutu. Ife tinatenga mipukutu,momwempukutu uwu unaperekedwera ku dzanja Lake. Momwekuti Yeremia, mu Yeremia 32:6, msuwani wake, Hanamieli,anamusiyira iye zodzalandira zina. Ndipo iwo anali akupita kuukapolo. Chimene, ife tikupita mmenemo, ndi iye, mmawa uno:ukapolo. Ndipo iwo unakasungidwa mu chotengera chadothi;kusonyeza kumene mphamvu ya Mulungu, ndi mipukutu ndizinsinsi za Mulungu, zimadziwidwira, mu mtima. Dongosololathu la chiwombolo, chimodzimodzi ziri nkusungidwa muzotengera zadothi, Dzina la Yesu ndi vumbulutso.

61 Ife tikupeza kuti uwu unasindikizidwa nazo ZisindikizoZisanu ndi ziwiri, ndipo Chisindikizo chirichonse chinalichitakutidwa mozungulira. Ndipo pamene vumbulutso linalikubwera, Iye ankasolola Chisindikizo, ndi kuchimasulaicho ndipo ankawerenga chimene Chisindikizo chimenechochinkanena. Ndiye Iye ankamasula chimodzi chotsatiracho,mpukutu, ndi kuwerenga chomwe Chisindikizo chimenechochinkanena. Kumasula china chotsatiracho, kukoka ichondi kuwona chimene Chisindikizo chimenecho chinkanena,ndi chimene vumbulutsolo linali. Ndizo chimodzimodzizomwe Zisindikizo zathu Zisanu ndi ziwiri, zomwe ife tikutitilowemo posachedwapa, ife tikudalira, zomwe ziti zidzachite.Chisindikizo chirichonse, pamene icho chikuchotsedwa paBukhulo, lidzakhala litafunyululidwa, ndipo izo zidzasonyezachimodzimodzi zomwe zinali zitachitika.

Page 16: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

16 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

62 Ife tikupeza kuti pali “zisanu ndi ziwiri,” zisanu mudongosolo la chiwombolo. Faifi ndi chiwerengero. Ndipo alipoma faifi asanu ndi awiri; Zisindikizo Zisanu ndi ziwiri, MizimuIsanu ndi iwiri, angelo asanu ndi awiri, Malipenga Asanu ndiawiri, ndi mibadwo ya mpingo isanu ndi iwiri. Kotero, inumukuona, mafaifi asanu ndi awiri ndiwo chisomo. Faifi ndiyochisomo, ndipo seveni ndiyo ungwiro. Kotero izo ziri mwangwirokumangoyenda chimodzimodzi basi, mwaona. Chabwino.

63 Monga, Chisindikizo chirichonse chitamatulidwa mu Mawua Mulungu, chimaulula kwa munthu wa m’badwowo, m’badwoumene ife tiri kukhalamo, mzimu wa m’badwo, mpingo wam’badwo. Chivumbulutso 10, pa mapeto, ife tikupeza pameneChisindikizo chotsiriza chinamatulidwa, ife tikumupeza Mngeloataimirira ali ndi phazi limodzi pa mtunda, ndi limodzipa nyanja, ali ndi manja Ake mmwamba Kumwamba, ndiutawaleza pamwamba pa mutu Wake, kulumbirira pa Iyeyemwe amakhala moyo kwanthawi ndi nthawi, kuti nthawiyatha, pamene Chisindikizo chotsiriza. Ndipo inu mudikirempaka ife tifike mu Zisindikizo zimenezo ndi kuwona kumeneChisindikizo chimenecho chiri. Inu mukatha kupeza makumiasanu ndi awiri a masabata, ndiye mudzawone kumeneZisindikizo ziri, “Nthawi yatsirizika,” chiwombolo chatha, Iyeali tsopano Mkango ndi Woweruza. Iye ali Mpulumutsi wanummawauno, koma tsiku lina Iye adzakhalaWoweruzawanu.

64 Ya 8 mpaka ku ya 1…ndime ya 14 ya mutu wa5, ikuwulula nthawi ya Mwanawankhosa kuti akhaleakupembedzedwa, Kumwamba ndi pa dziko lapansi komwe;Bukhu la zisindikizo zisanu ndi ziwiri, Mwanawankhosawoyenera, Wowombola Wapachibale. Ndipo kuyambira pandime ya 8, mpaka ku ya 14, Angelo akumupembedza Iye, akuluakumupembedza Iye, Zolengedwa Zamoyo zikumupembedzaIye. Ndipo Yohane anamupembedza Iye mochuluka kwambirimpaka iye anati, “Cholengedwa chirichonse Kumwamba,pa dziko lapansi, pansi pa dziko lapansi, chinandimva inendikuti, ‘Madalitso, ulemerero, mphamvu, nzeru, ukuluzikhale kwa Mwanawankhosa.’” Nthawi yakupembedzakwa Mwanawankhosa Mfumu. Tsopano, Mpingo wapita,kumbukirani.

65 Tsopano tiyeni titembenuzire ku Daniele, ndipo mutu wa9, ndi ndime za 1 mpaka 3. Ndiyeno ife tati titenge ya 20mpaka ya 27, chifukwa ili ndi pemphero chabe la Daniele. Inendikufuna inu kuti mukawerenge izi mobwereza bwereza, musabata lonseli, tsopano, mpaka inumutazimvetsa izo.

Mu chaka choyamba cha Dariyo mwana wa…mbewu yaAmedi, yemwe anamlonga ufumuwolamulirachigawo cha Akaldia;

Page 17: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 17

Mu chaka choyamba cha kulamulira ine Danieli… -mvetsa, ndinamvetsa mwa mabuku kuti chiwerengerocha…zaka, zomwe mawu a Mulungu anadza kwaYeremiya mneneri, kuti iye akanati adzakwaniritsezaka makumi asanu ndi awiri mu chipasuko chaYerusalemu.Tsopano (yotsatira) ine ndinaika nkhope yanga kwa

Ambuye Mulungu, kumfunafuna mu pemphero ndimapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa:…Ine ndinapemphera kwa YEHOVA…Mulungu,

ndipo ndinapanga kuvomereza kwanga,…66 Ndipo mopitiriza pitiriza iye akupita, mpaka tsopano ifetikufika ku ndime ya 20. Kuti tisunge nthawi, anthu aimirira,ine ndikufuna inu kuti mukafike pa 20, mpaka ife titsike pansitsopano ku—ku ndime ya 20.

Ndipo pamene ine ndinali chiyankhulire, ndikupemphera, ndi kuvomereza tchimo langa nditchimo la anthu a kwathu ku Israeli, ndi kuperekamapembedzero anga pamaso pa YEHOVAMulunguwangachifukwa cha phiri loyera la Mulungu wanga;Komabe, pamene ine ndinali ndikuyankhula mu

pemphero, ngakhale mwamuna Gabriele, yemwe inendinali nditamuwona mu masomphenya poyamba,anayamba…anayambitsa kuuluka mwaliwiro,anandikhudza ine pafupi nthawi ya kupereka nsembeya madzulo.Ndipo iye anandidziwitsa ine, ndipo anayankhula kwa

ine, ndipo anati, O Danieli, ine tsopano ndabwera kunokuti ndidzakupatse iwe luntha ndi kumvetsa.

67 Bwanji ngati ife tikanakhoza kokha kukhala tiri kumeneko!Kodi Iye anamupeza chotani iye? Mu pemphero.

Mngelo, “mwamuna.” Inu mukuzindikira, iye anamutchaIye, “mwamuna.” Ndipo pokhala wa…

Ndipo pakuyamba kwa mapembedzero anga, lamulolinadzapo, (ndipo linadza kuti iye azipita), ndipoine ndadza kuti ndidzakusonyeze iwe; pakuti iweuli wokondedwa kwambiri: ngati…chotero mvetsankhaniyo, ndipo lingalira masomphenyawo.Masabata makumi asanu ndi awiri atsimikizidwira

pa anthu ako ndi pa mzinda wako wopatulika,kapena mzinda wako, kuti amalizitse cholakwira,…kuti apange kutha kwa tchimo, ndi kuti apangechiyanjanitso cha kusaweruzika, ndi kuti abweretsemmenemo chirungamo chosatha, ndi kuti asindikizemasomphenya ndi uneneri, ndi kuti adzoze maloOpatulikitsa.

Page 18: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

18 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

Apo pali zifukwa zofutukuka pasanu ndi kamodzi za kudzaKwake. Tsopano zindikirani.

Tsopano, chotero, dziwa chotero ndipo mvetsa,(tsopano mvetserani) kuti kuyambira pa kuperekedwakwa kulamulira kuti abwezeretse ndi kuti amangeYerusalemu kufikira…Mesiya Kalonga adzakhala alimasabata asanu ndi awiri,…masabata sikisite thuu:ndipo msewu udzamangidwa kachiwiri, ndi makoma,ngakhale mu nthawi ya mavuto.…atapita masabata sikisite thuu Mesiya

adzadulizidwa, koma osati chifukwa cha iyemwini:ndipo anthu a kalonga yemwe ati adzadze—kalongayemwe ati adzadze… kuwononga mzinda ndimalo opatulika; ndipo mapeto ake adzakhala ndichigumula,…kufikira ku chimariziro cha nkhondochipasuko chiri chotsimikizika.Ndipo iye adzatsimikizira pangano (mvetserani)

ndi ambiri kwa sabata limodzi, limodzi la seventeya masabata awa: ndipo mkati mwa sabata iyeadzapangitsa nsembe ndi…zofukiza kuti zithe, ndipa kusefukira kwa zonyansa iye adzazipanga izochipasuko, ngakhale kufikira ku chimariziro, ndipoicho chotsimikizidwiracho chidzatsanuliridwira paopasulidwawo.

68 Tsopano, pamenepo pali phunziro lathu la msonkhanowathuwotsatirawachitatu, chinai, chisanu, chirichonse chimeneAmbuye ati aulule. “Sevente ya masabata.”69 Tsopano, ine ndimufunsa Doc, ngati iye angalole, usikuuno,kuti aimike bolodi langa apo, kotero kuti ine ndikhozekumazilemba izo pamenepo. Ine sindikufuna inu kutimuziphonye izo. Tsopano inu muyenera kuti muziphunzirandi ine, ndi kuphunzira mwakuya, kapena inu mudzaziphonyaizo. Ndipo ine ndikufuna kuti ndizijambule izo apa pano pabolodi lakuda, ndiyeno inu mukabweretse mapensulo anu ndipepala ndipo muzilemba masiku amenewa, nthawi izi, ndi zonseza izo.70 Tsopano, sevente ya sabata akuyamba (tsopano mvetsaniizi) Mpingo utachotsedwapo kale. Tsopano, aliyense yemweakumvetsa zimenezo, anene, “Ameni.” [Osonkhana akuti,“Ameni.”—Mkonzi.] Tsopano,Mpingo utachotsedwapo kale.71 Chivumbulutso 6:1, mpaka Chivumbulutso 19:21, ndizolumikizana ndi sevente ya masabata, chotero ife tiyenerakuima ndi kufotokoza, ife tisanati tipite patsogolo. Ife tiyenerakuima ndi kufotokoza chifukwa chakemakumi asanu ndi awiri amasabata awa. Chifukwa, ngati inu simutero, inu mudzaphonyaZisindikizo zimenezo, inu mudzaphonya Malipenga amenewo,inu mudzaphonya Mbale zimenezo, Miliri imeneyo, mizimu

Page 19: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 19

itatu yosayera imeneyo yonga achule, Matsoka atatu amenewo,kuponyedwa kunja kwa chinjoka chofiira, mkazi mu dzuwa.Inu mudzaphonya izo zonse, ngati inu simutero, chifukwa izozikuchitika umu momwe mu sabata lachi makumi asanu ndiawiri ili. Ndi pamene izo ziri kuchitika.72 Tsopano, mneneri Danieli anakhala ali mu Babeloni kwazaka sikisite eyiti. Inu amene mukufuna kuti mufufuze ndizina mmbuyo, ndi kuzisungira nokha ina ya nthawi, imeneine ndakhala nayo pa—kuyang’ana izo. Zaka sikisite eyiti! Iyeanapita mu ukapolo mu b.c. 606, ndipo pamene masomphenyaanabwera kwa iye inali—inali b.c 538. 538 kuchokera mu606, zikusiya sikisite eyiti. Zaka sikisite eyiti iye anakhala alimu Babeloni, pakati pa achikunja, ndi kukhala ali nachobechigonjetso. Ameni. Ife sitingakhoze kukhala ora.73 Koma iye anakhala ali pakati pomwe, wopanda aliyensekoma amzake atatu, ndipo iwo ali mmagawo osiyana aufumuwo. Koma, Danieli, akuima yekha ndi Mulungu, anagwirachigonjetso kwa zaka sikisite eyiti. Taganizani za izo! Inesindikufuna kuti ndiyambe kulalikira, chifukwa ili likuyenerakuti likhale Uthenga wophunzitsa. Koma, zaka sikisite eyiti, iyeanali atasunga chigonjetso ndipo anali wosaipitsidwa, pamasopa Mulungu; wopanda ubatizo wa Mzimu Woyera, wopandaMagazi a Yesu Khristu kuti amupangire iye chitetezero; ali nawokokha magazi a ng’ombe, ndi mbuzi, ndi nkhosa, zomwe iyeankachita kumazipereka mwamseri, chifukwa cha miyambo yachikunja ya mdziko limenelo. Iwo anali atatengedwera kupitakumeneko. Yeremia analosera za iwo, kuti iwo anali kupitakumeneko.74 Tsopano, Danieli, o, mai, iye anali atayamba kuwona kutinthawi inali kuyamba kuyandikira, basi monga ife tiri lero.Danieli anayamba “kumvetsa,” iye anati, “mwa kuwerenga kwamabuku.”

Ndipo mu chaka choyamba cha ulamuliro wa…Danieli…mu ulamuliro ine Danieli ndinamvetsa mwamabuku chiwerengero cha…zaka, chotero…mawu aYEHOVA anadza kwa Yeremia mneneri, zomwe ziyenerakuti zikwaniritsidwe zaka makumi asanu ndi awirimu…chipasuko cha Yerusalemu.

75 Yeremia, mu b.c. 606, ananenera, chifukwa cha machimoawo ndi kupanda umulungu, kuti iwo akanati adzakakhale zakamakumi asanu ndi awiri.76 Inumukukumbukira, panali mneneri wina yemwe anabweramu tsiku limenelo. Ine sindingakhoze kumutchula dzina lakepa nthawi ino. Ine ndikhoza kukugwirirani inu ilo mu—mumaminiti pang’ono, ngati ine nditati ndiyang’ane mmbuyo kwakanthawi. Koma iye anabwera uko ndipo anati, “Yeremia, iwe

Page 20: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

20 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

ukulakwitsa. Mulungu akasunga Israeli kumeneko kwa masikuakuti okha, kwa akuti, pafupi zaka ziwiri.”77 Yeremia anati, “Izo zikhale chomwecho. Ameni.” Iye anati,“Koma dikirani miniti. Tiyeko iwe ndi ine tifufuzane wina ndimzake, monga aneneri.” Iye anati, “Kumbukira, akhalapo iwoamene ananenera tisanakhalepo ife, ndipo iwo ananena zinthuzomwe zinali zolakwika. Ndipo Mulungu anathana nawo iwochifukwa cha kunena zinthu zolakwika. Chotero, tiyeko ifetikhale otsimikiza. Koma Ambuye Mulungu wandiuza ine kutiziripo zakamakumi asanu ndi awiri panobe.”

Mulungu anamukantha mneneri wabodza ameneyo, ndipoanachotsa moyo wake chaka chomwecho, chifukwa Mulunguanali atamuuza mneneri woona uyu kuti zinalipo zaka makumiasanu ndi awiri.78 Ndipo ine ndikufuna inu kuti muzindikire momwe Danieli,komabe ali mlendo, komabe atachotsedwa kwa anthu ake,atachotsedwa kwa mpingo wake, wopanda msonkhano umodziwa mpingo, wopanda mpingo uliwonse woti azipitako, wopandanyimbo zirizonse kuti ziyimbidwe kupatula zomwe iye analikuziimba yekha, mkati mwa izi zonse, komabe anagwiritsamopitirira ku chimene mneneri ameneyo ananena. Ameni!Ameni!79 Wopanda mpingo woti azipitako, wopanda munthu wochitanaye chiyanjano; aliyense ankapita ku akachisi achikunja,aliyense ankapembedza mafano awo. Kopanda nyimbo zaChikhristu; popanda wina ankakhulupirira chinthu chomwechochimene iye anali. Ndipo mu zaka sikisite eyiti, kuchokera alimnyamata wa usinkhu wa pafupi zaka khumi ndi ziwiri, khumindi zinai, pamene iye anatengedwa kupita uko, iye anagwiritsamoona kwa Mulungu; ndipo anamvetsa mwa mneneri Yeremiakuti masiku anali pafupi kuti akwaniritsidwe.

Momwe izo zikanati zichenjezere mtima wa mneneri woonaaliyense wa Mulungu lero, kuti ife tiyang’ane mmbuyo ndikuwona chimene mneneri woona uyu ananena, ndi kudziwa kutiife tiri pa nthawi yotsiriza.80 Iye anati, “Ine ndinamvetsa mwa mabuku kuti Yeremia,m’bale wanga, zaka zambirimbiri zapitazo, ananenera kutiIsraeli akanati adzakhale kumusi kuno zaka makumi asanundi awiri. Ndipo nthawi imeneyo ili pafupi kukwaniritsidwa.”Ndipo iye anadzipanga yekha kukonzeka. Ndipo iye anaitanitsakusala, ndipo iye anadziyeretsa yekha, ndipo pamene…mapulusa ndi ziguduli, ndipo anaziyika izo pamutu wake, ndipoanayamba kusala ndi kupemphera, kuti amvetse za tsiku limeneiwo anali kukhalamo.81 Ndipo ngati Danieli, mneneri wa Ambuye, akanakhozakufunsira mu mabuku a Yeremia, ndi kumufikitsa iye pa malooterowo; kuti ngakhale Israeli kutuluka, onse a iwo amoyo,

Page 21: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 21

anali kutuluka kuchokera mu Babeloni, kuti abwerere ku dzikola kwawo, zikanati zimupangitse iye kuti asale ndi zigudulindi mapulusa. Ndi mochuluka bwanji momwe izo ziyenerakuti zichite kwa Mpingo wa Mulungu wamoyo, podziwa kutinthawi ikuzilala ndipo siidzakhala iliponso; ndipo Kudza kwaAmbuye Yesu Khristu, ndi Zakachikwi zazikulu ziri zokonzekakuti zilowe mmenemo! Ife tingakhoze bwanji kutaya nthawiyopanda-kutayika, njuga, dzenje losambirapo Lamlungu,opanda nthawi ya kwa Ambuye? Basi kumangothamangathamanga…Ngati m’busa ayankhula pa chinthu chinachakechimene iwe suli kuchikonda, iwe umaimirira ndi kutulukapanja. Ndipo ngati—ngati mpingo ukhala motalikitsa kwambiri,bwanji, iwe—iwe, iwe—iwe uli wosakhutitsidwa. Tayang’ananipa chikhalidwe chathu. Taonani chimene ife tiri nkuchita.

Fanizitsani miyoyo yathu ndi mneneri ujayu. Munthummodzi, mu ufumu wathunthu, wopanda mpingo wotiazipitako, ndipo wopanda kulikonse koti azipitako. Iyo inaliitagwetsedwa pansi ndi kuwotchedwa nkugwa; mzinda wake,anthu ake anali mu nsinga. Zaka sikisite eyiti! Sikisite eyiti,sikisite naini, makumi asanu ndi awiri; iye anali nazo zakaziwiri zotsalira. Chotero pamene iye anayamba kuwerenga mubukhu ndi kuwona kuti nthawi inali kuyandikira pafupi kutizikwanire, zikhale zitakwaniritsidwa, iye anapita kwa Mulungumu pemphero, kuti afufuze za izo.82 Ndi nthawi bwanji! Kodi ife tikuchita chiyani? Pamene,“Mafuko akusweka; nyanja ikukukuma; mitima ya amunaikulephera mwa mantha; zododometsa za nthawi.” Zinthuzonse izi ndizo, cholembedwa cha pa khoma. Kuphwasuka kwamitundu; mitundu yonse ya zoipa ziri kuchitika mu dziko;ndi makangano, ndi ndewu, ndi kupsyerana mtima. Ndi zidazitapachikidwa mopachikira, fuko limodzi laling’ono ilo lakukula kwa Cuba kumusi kuno likhoza kuwononga dzikoli mumaminiti khumi. Ndipo iwo akukangana wina ndi mzake, anthuopanda umulungu omwe samudziwa Mulungu ndipo saidziwamphamvu Yake.

Ndipo Mzimu Woyera mu Mpingo, ukusuntha pakati paOsankhidwa, akudzisonyeza Iyemwini wamoyo zitatha zakazikwi ziwiri, kuti Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. Ife tingakhoze bwanji kungokhala olobodoka? Ifetingakhoze bwanji kumangothamanga pamwamba pa izo? Ndinthawi ife tikanati tizifufuza, kuyang’anira ora lalikulu ilolimene likuyandikira.83 Tsopano, iye anawerenga mu Yeremia, mutu wa 25. Tiyenititembenuzire uko mu Yeremia, mutu wa 25, ndipo tiwerengezimene Yeremia anali nazo kuti anene. Makamaka, tiyenitiyambire pa ndime ya 8, chifukwa ndi…ine ndikufuna inu kutimutsimikize kuti muzimvetse izo. Ndime ya 11 ndi pamene ine

Page 22: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

22 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

ndinali nditalemba pano kuti ndiwerenge, koma tiyeni tiyambirepa ndime ya 8.

Chotero pakuti atero YEHOVA wa makamu;…Ine ndikungozikonda zimenezo. Pamene ine ndingakhoze

kumumva mneneri akuimirira ndi PAKUTI ATERO AMBUYEMULUNGU, m’bale, ndi zimenezo. Kwa ine, izo zimakhazikitsaizo. Ndizo zonse za izo.

…pakuti atero YEHOVA wa makamu; Chifukwa iwesunamve mawu anga,Taona, ine nditumiza ndi kutenga mabanja onse aku

mpoto, atero YEHOVA, ndi Nebukadinezara mfumu yaBabeloni, wantchito wanga, ndipo adzawabweretsa iwokachiwiri…motsutsa dziko lino, ndi motsutsa okhalammenemo, ndi motsutsa mafuko onse kozungulirakwake, ndipo ine ndidzawawononga iwo psyiti,…Kumbukirani, awo anali osankhidwa a Mulungu amene

Iye akuwakamba. Amenewo sanali achikunja. Amenewo analimamembala a mpingo.

Kuwonjezera apo ine ndidzatenga kuchokera kwaiwo liwu la chisangalalo,…liwu la kukondwa, (basimonga ife tiri nazo lero, gwedemula yense, Ricky ndiElvis,) ndipo, o, liwu la mkwati,…liwu lambalame…kapena, mkwatibwi, kani, phokoso la mwala wamphero,…kuwala kwa muni.Ndipo dziko lonse ili lidzakhala bwinja,…

Mvereni mneneri ameneyo akufuulira, “Dziko lonse ililidzakhala liri bwinja!” Ndipo osati kuti timusanzire wantchitowamkulu uyu wa Mulungu, koma ine ndikunenera kuti fukolonse ili lidzakhala liri bwinja. Mulungu adzalanga fuko linochifukwa cha machimo ache. Ngati Mulungu sakadamulolaIsraeli, osankhidwa Ake, Mbewu ya Abrahamu, omwe Iyeanapangana pangano ndi lonjezo nawo, ngati Iye sakanawalolaiwo kumapitirira ndi kachitidwe koyipa; ngakhale iwo analiachipembedzo mpaka pakati, anali nayo mipingo yayikulu,ndi ansembe, ndi marabbi; koma chifukwa cha makhalidweoipa ndi zinthu pakati pawo, ndipo Mulungu anawapanga iwokukolola zimene iwo anazifesa, chomwechonso ife tidzalandiraizo. Ndime ya 11:

…dziko lonse ili lidzakhala bwinja, ndi…chodabwitsidwa;…Izo ndizo, aliyense kumangoyang’ana ndi kumati, “Ndi awo

pamenepo. Iwo anali aakulu kwambiri. Tayang’anani pa iwotsopano.”

…ndipo mafuko awa adzatumikira mfumu ya kuBabeloni zaka makumi asanu ndi awiri.

Page 23: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 23

Iyo ndiyo nthawi ya moyo. Ndi pamene akale anu, amayiodala achikulire anali khanda. Iwo anali mkati mmenemoopanda Mulungu, opanda mpingo, opanda nyimbo, opandachirichonse, kwa m’badwo wathunthu, kufikira m’badwo wonsewochimwa umenewo utatha kufa.

Ndipo zidzafika pochitika kuti, pamene zaka makumiasanu ndi awiri zidzakhala zitakwaniritsidwa, kuti inendidzalanga mfumu ya Babeloni, ndi fuko limenelo,atero YEHOVA, chifukwa cha kusaweruzika kwawo, ndidziko la Alkadia, ndipo ine ndidzalipanga ilo bwinjalopitirira.Ndipo ine ndidzabweretsa pa dziko limenelo mawu

anga onse amene ine ndakhala nditanena motsutsa ilo,ngakhale onse amene alembedwa mu bukhu ili, limeneYeremia walosera motsutsa fuko lonse.Pakuti mafuko ambiri ndi mafumu aakulu

adzadzitumikira okha—okha a iwo nawonso: ndipoine ndidzawabwezera…molingana ndi ntchito zawo,ndi molingana ndi mawu awo a manja awo omwe.Pakuti atero YEHOVA Mulungu wa Israeli kwa ine;

Tenga chikho cha vinyo wa ukali pa dzanja langa, ndipoupangitse mafuko onse, kumene ine nditi ndidzakutumeiwe, kuti akamumwe iye.Mwa kuyankhula kwina, “Yeremia, ine ndakupatsa iwe

uthenga uwu. Usati ungokhala duu. Usati ukhale mu maloamodzi, koma nenera ku mafuko onse.” Kodi inu mukutsatiraizi? [Osonkhana akuti, “Ameni.”—Mkonzi.] “Nenera kwa fukolonse. Sonyeza zizindikiro Zanga ndi zodabwitsa, ndipo aloleiwo adziwe kuti ine ndikubwera kuti ndidzachite izi.”

Ndipo iwo adzamwa, ndi kukhala dzandidzandi, ndikukhala openga, chifukwa cha mawu omwe ine nditindidzawatumize pakati pawo.

84 Kodi iwo akuchita chiyani mu tsiku lomwe lino?Iwo amakutcha iwe—mneneri wabodza, kukutcha iwe—wonyengerera, kukutcha iwe—wotentheka, wamaula, kapenawolota wa maloto, kapena mtundu wina wa wowerengamaganizo. “Iwo adzakhala openga!” Ndipo mawu akuti openga,ngati inu muti mudzawaswe iwo, amatanthauza “misala.”“Iwo achita misala kwenikweni, ndi kumati, ‘Nha, musaperekechidwi chanu kwa woyera wodzigudubuza ameneyo, zamkhutuzimenezo,’ chifukwa cha Mawu omwe ine nditi ndidzawatumizepakati pawo.”85 Inu mukuona mbiriyakale ikudzibwereza yokha? Yeremiasakanati agwirizane nawo Afarisi amenewo, Asaduki,Aherodia, chirichonse chimene iwo akanati akhale. Iye, iyeanangowatulutsa Mawu kunja, ndipo Iwo anawapanga iwo onsekupengera pa iye. Chiyani? Tsopano zindikirani.

Page 24: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

24 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

Ndipo ndiye ine ndinatenga chikho pa dzanja laYEHOVA, ndipo ndinapangitsamafuko onse kuti amumweiye,…Yeremia sanakhale kunyumba. Yeremia sanangokhala pa

malo amodzi aang’ono, koma iye anapangitsa mafuko onsekuzimwa izo.

…kwa omwe Yehova ananditumiza ine:86 Yeremia anatenga Mawu a Yehova, vinyo wa Mawu Ake.Ndipo vinyo ali mphamvu ya Mawu Ake. Vinyo ali nayomphamvu. Vinyo ali choledzeretsa. Vinyo ali nayo mphamvupaseri pake. “Ndipo ine ndinatenga Mawu a Yehova,” anateroYeremia, “ndipo ndinawapangitsa Iwo kuwonekera. Vinyo,mphamvu yomwe ili mwa Iye, ine ndinaichititsa pamaso pa iwo,ndipo iwo samakhoza kuwamvera Iwo.”

Mulungu anati, “Ndiye ine ndiwatumiza iwo kwa zakamakumi asanu ndi awiri mu Babeloni.” Basi ndicho chimene Iyeanachita. Olungama ndi osalungama anapita, mofanana.87 Tsopano, tibwerere ku phunziro. Danieli anakhalaakuwerenga. Tangoganizani, Danieli ankawerenga Mawuomwewa amene ife tiri kuwawerenga mmawa uno. Danieliankawerenga Baibulo lomweli, mopumira momwemu, ziganizozomwezi, zinthu zomwezi zomwe ine ndiri, mwa thandizola Mulungu, ndikuwerengerani inu mu Mauthenga otsatiraangapowo, chinthu chomwecho, kuti ndikusonyezeni inu kutiife tiri pa nthawi yotsiriza.

Ndipo Danieli, atatenga Mawu kuchokera kwa Yeremia,anapita uko ku Babeloni. Ndipo iye anali mneneri wodzozedwa.Ndipo iye ankachita zozizwitsa, chizindikiro, amakhozakutanthauzira malirime osadziwika, ndipo anachita zizindikirondi zodabwitsa pakati pawo. Komabe, akuima yekha, paiyeyekha! Ameni! Iye anaima yekha.88 Koma Yeremia anali atawalemba Mawu awa, zakazambirimbiri zisanachitike. Ndipo Danieli, akutanthauziraMawu, anapeza… “Anati, tsopano dikirani miniti. Ifetikubwera moyandikira ku nthawi yotsiriza, pakuti inendakhala kale ndiri kuno zaka sikisite eyiti. Ndipo mneneri waAmbuye,” ameni, “m’bale wanga, mneneri woona wa Mulunguyemwe anadzitsimikizira yekha mneneri, ananenera kwa ife.Ine ndiri nazo izo zolembedwa pano mu bukhu, pomwe akuti,‘Zaka makumi asanu ndi awiri zidzakwaniritsidwa.’ O AmbuyeMulungu, ife tikuyandikira mapeto. M’badwo wonse uja ulinkufa nutha. Kodi Inu muchita chiyani tsopano, Ambuye? Inumunalonjeza kuti mutitumizira ife…” Ndipo iye anadziyikayekha mu dongosolo, kuti azipemphera.89 O Mulungu, ngati inayamba yakhalapo nthawi yomwe ifetimayenera kumadziyika tokha mu dongosolo, kuti tipemphere,ndi pakali pano. Chifukwa, ife monga antchito Ake owona,

Page 25: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 25

ife tikuwona, mwa Zolemba za atumwi, mwa zochenjeza zaMzimu Woyera, kuti ife tiri mu tsiku lotsiriza. Mzimu Woyeraukuyankhula Izo. “Mu masiku otsiriza, amuna adzakhalaammutu, amaganizo apamwamba, okonda zosangalatsa kuposaMulungu, okuswa pangano, onenera zabodza, osadzigwira, ndionyoza iwo amene ali abwino.” Ine ndikumvetsamwaKalata.90 Ndipo ine ndikumvetsa kuti kudzabwera onyoza, mutsiku lotsiriza. Ine ndikumvetsa kuti kudzakhala kuli fukolikutsutsana ndi fukolo, mu tsiku lotsiriza. Ine ndikumvetsakuti kudzakhala kuli mafunde osefukira, mu tsiku lotsiriza.Ine ndikumvetsa kuti kudzakhala kuli zooneka mowopsya,monga mbale zowuluka, mmwamba, zowoneka mwachinsinsi,ndipo mitima ya amuna idzakhala ili kulephera chifukwacha mantha. Kudzakhala kuli kunyumwitsa kwa nthawi, ndikukwiirana pakati pa anthu. Ine ndikuwerenga kuti iwo onseadzapita mu mabungwe ndi zipembedzo, ndi kukhala nachochitaganya, mu tsiku lotsiriza. Ine ndikumvetsa kuti akaziazidzadula tsitsi lawo mu tsiku lotsiriza. Ine ndikumvetsa kutiiwo azidzavala zovala zazifupi, ndi kumayenda ndi nsapatozazidendene zazitali, akudzigwedeza pamene iwo akuyenda, mutsiku lotsiriza. Ine ndikumvetsa kuti makhalidwe adzakhalaali otsika kwambiri mu tsiku lotsiriza. Ine ndikumvetsa kutialaliki adzakhala ali abusa abodza mu tsiku lotsiriza, omweati azidzanyengerera, ndipo sadzati azidzawadyetsa anthuMawu a Mulungu, koma azidzapita natsatira tizikhulupirirondi zinthu, mmalo mwake. Koma ine ndikumvetsa kutikudzakhala kuli Liwu liti lidzabwere mu tsiku lotsiriza,likufuula kuchokera ku chipululu, likuwaitanira anthu kutiabwerere ku Uthenga wapachiyambi, kubwerera ku zinthu zaMulungu. Ine ndikumvetsa, mwa Bukhu, kuti zinthu zimenezozidzachitika.91 Ine ndikumvetsa kuti mu masiku otsiriza uko kudzabweranjala. Mipingo idzakhala ili mwabungwe kwambiri, ndiokhazikika chotero ndi chirichonse, kuti mu masiku otsirizauko kudzabwera njala, ndipo iyo sikuti idzakhala ya mkatendi madzi okha, koma ya kumva Mawu owona a Mulungu.Ndipo anthu azidzapita kuchokera kummawa, kuchokerakumadzulo, kuchokera kumpoto, ndi kummwera, akufunafunakuti amve Mawu owona a Mulungu. Koma mipingo idzakhala ilimwabungwe kwambiri ndi omangika, mwakuti iwo adzalepherakuti awamvetse Iwo. Ine ndikumvetsa izo mwa Mabuku. Koma,mu tsiku limenelo, O Mulungu, kudzakhala kuli Nthambi itiidzawuke kuchokera kwa Davide.92 Ine ndamva kuti Iye adzatumiza Eliya tsiku limenelolisanafike pa nthawi yotsiriza, ndipo iye adzakhala nawoUthenga umene uti udzatembenuze mitima ya ana kubwererakwa makolo, kuitembenuza iyo kubwerera ku chapachiyambi,kupitanso mmbuyo kumapeto, ndi kukayamba. Ine ndamva kuti

Page 26: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

26 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

izo zidzachitika basi Mzimu usanati usiye mpingo waAmitundu,kuti ubwerere kwa Ayuda.93 Ndipo ine sindikumvetsa kokha mwa Kalata yokha. Inendikutero mwa Mawu, mwa Mawu olembedwa, kuti Israeliadzabwerera ku dziko la kwawo; ndipo ine ndikumuwona iyeakukalowa mmenemo.94 Ine ndikumvetsa mwa Makalata, a aneneri, kuti Israeliadzakhala fuko. Iwo adzakhazikitsanso kupembedza kwamkachisi. Mulungu adzapita kukachita ndi iye kachiwiripamene iye akubwera ku dziko la kwawo. O! Aneneri awiriadzawuka mu masiku otsiriza, ndi iwo. Ine ndikumvetsazimenezo. Basi pamene Mpingo wa Amitundu ukusunthakuchokapo, aneneri awiri adzafika, Elisha ndiMose, kwa Israeli.Ife tidzazitenga izo pamene ife tikumka tikudutsa.95 Mneneri anawona kuti nthawi inali pafupifupikukwaniritsidwa kumusi ukomuBabeloni. Chabwino.96 Gabrieli akutulukira, kuti awulule osati kokha chimene iyeanali kuchipempha, koma kuti amuwuze iye njira yonse mpakaku chimene chinatsimikizidwira kwa mtundu wa Ayuda, njirayonse mpaka ku chimaliziro. Ameni! iye anafunsa pang’onopokha, ndipo anapeza chinthu chonsecho. Iye anapempha kutiangodziwa…97 Danieli anali akuyesa kuti azindikire, “Utali wochulukachotani, Ambuye, ziti zikhale tsopano? Yeremia mneneri,wantchito Wanu, m’bale wanga, anali atanenera zaka sikisiteeyiti zapitazo, ndipo anati, ‘pali zaka makumi asanu ndi awirizomwe anthu awa ati akhale ali kuno.’ M’badwo wonse wakalezachitika kuti wapita tsopano.”98 Ulipo m’badwo wakale wa chipentekoste umene unawuka,zaka makumi anai zapitazo. “Ankhondo akale,” iwo analikutchedwa. Iwo anapanga bungwe, ndi kumenya, ndikukangana, monsempaka kupyola Phiri la Horebu ndi Nebo, ndikudutsa kumeneko. Koma, potsiriza, ife tiri pa mtsinje tsopano.Iye akuti awukitse wina watsopano, ndi Yoswa kuti awatengenawawolotse iwo. Lamulo linalephera; Mose anapita nalo ilo;Mose analephera. Yoswa anawatenga nawawolotsa iwo. Ifetikupeza kutimabungwe alephera, komaMzimuwaMulungu…Yoswa, mawu akuti Yoswa, amatanthauza “Yesu Mpulumutsiwathu.” Kuti, Mzimu Woyera udzabwera mu Mpingo. Osatibungwe, koma Mzimu Woyera udzafika pakati pa anthu ndikuupanga Iwo kukonzekera kuti uzipita chokwera, kuwolokaYordani. Ine ndikumvetsa mwa kuwerenga kwa Bukhu kutindicho chimene chiti chichitike. Ndipo Mulungu akudziwakuti ndicho chimene ine ndikufunafuna tsopano, kuti inendikhoze kuwatonthoza anthu Ake ndi kuwauza iwo chimenechayandikira, konse kuno mmawa uno, ndi kunja kudutsa mu

Page 27: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 27

maiko kumene matepi awa ati adzapite, mdziko konsekonse,kuti ife tiri pa mapeto a nthawi.99 Iye anaulula njira yonse mpaka Ufumu utabwezeretsedwakwathunthu ndi Zakachikwi zitayambika. Umenewo unaliuthenga wa Gabrieli. Iye anati, “Ine ndabwera kuti ndidzakuuzeiwe kuti ziripo makumi asanu ndi awiri za zaka, makumi asanundi awiri a masabata, panobe, zatsimikizidwira pa anthu ako,zatsimikizidwira mpaka ku mapeto kwa m’badwo wa Chiyuda.Alipo makumi asanu ndi awiri a sabata.” Tsopano penyanichimene Iye ananena. Kuti tsopano, kuchokera pa kupita ukokuti abwezeretse…

Makumi asanu ndi awiri a masabata atsimikizidwirapa anthu ako ndi pa mzinda…wako,…“Mzinda wako.” Babeloni sunali mzinda wake. Ndani…

Unali kuti mzinda wake? Yerusalemu.100 Tsopano, pamene ife tifika ku—chachisanu ndi chiwiri,kapena chitsimikiziro chofutukuka pasanu ndi kamodzi, ifetipeza chomwe mzinda umenewo uli, ndi kuwubweretsa iwopansi ndi kutsimikizira yemwe iye anali, yemwe anawuyambitsaiwo, kumene iwo unachokera. Utali wamomwe iwo uti udzaime?Kodi iwo udzamangidwanso kachiwiri? Mu nthawi yanji? O,zinthu zazikulu zasungidwira kwa ife. Chabwino.

Makumi asanu ndi awiri a masabata atsimikizidwirapa anthu ako ndi pa mzinda…wako, kuti atsirizecholakwira,…Tsopano, Iye sikuti anati, “Daniele…” Palibe kukaika

koma zomwe Iye anamuwuza iye kuti makumi asanu ndiawiri a masabata anali…Ine ndikutanthauza, zaka makumiasanu ndi awiri zinali pafupi kutha. Sikisite eyiti, kuperewerazaka ziwiri zokha. Ndipo ife tikupeza apo kuti uneneri waYeremia unagunda chimodzimodzi basi molondola. Zaka ziwirikenako, iwo anatuluka. Nehemia anapita ndipo anakatengaulamuliro kuchokera kwa mfumu, ndipo anamanga khoma munthawi yovuta. Iwo anagwira ntchito. Iye anati, “Khoma…”Mvetserani ku izi.

…kutsirizitsa cholakwira,…kupangitsa mapeto atchimo,…“Kuti apangitse mapeto a tchimo.” Kwa ndani? Ayuda.

“Zatsimikizidwira pa anthu ako,” osati pa Amitundu. “Pa anthuako,” Ayuda. “Ndi mzinda wako,” osati New York, osati Boston,Philadelphia, Chicago, Los Angeles, Roma. Koma, “Pa mzindawako,” Yerusalemu.

…ndi kuti atsirizitse cholakwira,…kupangitsamapeto a tchimo,…kupanga chiyanjanitso chakusaweruzika, ndi kuti abweretse mmenemochilungamo chosatha, ndi kuti asindikizemasomphenya

Page 28: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

28 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

ndi uneneri, ndi kuti adzoze Opatulika kwambiri.(Penyani!)Dziwa chotero ndipo zindikira, kuti kuchokera pa

kuperekedwa kwa lamulo kuti abwezeretse ndi kutiamangenso Yerusalemu (umene unali mzinda wake)mpaka…Mesiya Kalonga adzakhala ali asanu ndiawiri (a makumi asanu ndi awiri) masabata,…

101 Dikirani mpaka ife tidzalowe mu zimenezo! O, mai!Ndilo dalitso limene ine…Ine ndikadzipezera chingwe ndikudzimanga nacho ndekha pa malo ano.102 Anaulula izo njira yonse mpaka mmusi, anati, “Ine sikutindikuuza kokha iwe tsopano kuti zaka ziwiri izo ziri pafupibasi, izo zidzakhala zitatsirizika, kukwaniritsidwa.” Ndipo ifetonse tikudziwa kuti iwo chimodzimodzi anakakhala kumenekozaka makumi asanu ndi awiri, ndipo—ndipo anatuluka,chimodzimodzi basi zomwe mneneri ananena. Ndipo Yesaya,kapena ine ndikutanthauza…Danieli anamukhulupiriramneneri ameneyo, kotero pano iye anali, wokonzeka. Chabwino.Ndipo iye…103 Ndipo tsopano, pamene Gabrieli anabwera, Iye anati,“Ine ndabwera kuti ndidzakusonyeze iwe njira yonse, kutindidzaulule kwa iwe zinthu izi, kuti, njira yonse mpaka kuchimaliziro.” Mwaona? Penyani.

…chotembereredwa iye adzachipanga icho kukhalabwinja, ngakhale mpaka ku chimaliziro,…

104 Chimaliziro chiri “mapeto a zinthu zonse.” “Ine ndatindikusonyeze iwe zomwe ziti zidzachitike.” Tsopanomvetserani.Imvani izo! “Ine…Danieli, ine ndachita kutumidwa. Ndiwewokondedwa Kumwamba. Ndipo ine ndinawamva mapempheroako ndipo ine ndabwera pansi tsopano kuti ndidzakuuze iwezomwe zatsimikizidwira kwa Ayuda ndi Yerusalemu, kuchokerapakali panompakamapeto a chimariziro, chinthu chonsecho.”105 Tsopano, kodi inu mukumvetsa, kalasi? Ngati ife tingakhozekupeza chomwe makumi asanu ndi awiri a masabata awa ali, ifetidziwa pamene chimariziro chiri. O, mai! Mulungu atithandizeife kuti tidziwe izo. Iwo akutiuza ife chimodzimodzi penapakemu masamba awa, chimodzimodzi kuchokera nthawi imeneyokufikira nthawi ino, mpaka chimariziro, ndipo iwo saziphonyaizo miniti imodzi.106 Momwe Mawu aakulu a Mulungu…Pamene Mulunguanapanga dziko lapansi ndi kuliyika ilo mu kanjira.Ndipo ine ndinali kulalikira usiku wina, Lamlungu usiku,momwe kuti palibe kanthu kamalephera. Bwanji, dziko linolimatembenuzika mwangwiro chotero mpaka iwo akhozakukuuzani inu chimodzimodzi pamene dzuwa ndi mwezi zitizidzadutse, mu zaka makumi awiri kuchokera lero, mpakaku miniti yeniyeni. Ine sindingakhoze kukuuzani inu, mwa

Page 29: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 29

chidutswa chowonera nthawi chirichonse chimene ife tirinacho mu dziko; icho chingataye maminiti awiri kapena atatupa mwezi, kapena kupindula maminiti awiri kapena atatu,chopambana chimene ife tiri nacho. Ife sitingakhoze kupangakalikonse kangwiro chotero. Chifukwa, pali chinthu chimodzichokha changwiro, ndicho Mulungu. Ndipo Mulungu ndi MawuAke ali zofanana, koteroMawu aMulungu ali angwiro.107 Ndipo ngati ife tingakhoze kuwapeza masiku amenewa,ife tidzapeza chimodzimodzi pamene chimaliziro chitichidzakhale. Kodi inu mukuzimvetsa izi? [Osonkhanaakuti, “Ameni.”—Mkonzi.] “Izo zatsimikizidwira mpaka kuchimaliziro.” Ndime ya 24, “anthu ako ndi mzinda wakowoyera,” umene uli Yerusalemu. Ndiri ndi ya 21…ndime ya 24pano. Yesu ankalozera ku izi muMateyu 24.108 Tsopano, M’bale Collins, ngati iye ali pano mmawa uno,ine sindikudziwa ngati iye alipo kapena ayi. Mu mafunsousiku wina, iye anafunsa funso. (Ine ndikuganiza zonse ziribwino kuti ine ndinene izo, M’bale Collins.) Lokhudza, “‘Themberero limene likupanga chipasuko,’ mwaona, zimene ichochimatanthauza?”109 Yesu anayankhula za izo, mu Mateyu mutu wa 24, ndipoife tikuzipeza. Eya, Mateyu 24:15. Tsopano ndiroleni inendingotenga izo mwamsanga ndithu, chotero inu mukhozekuwona chimene, Yesu akuyankhula za chinthu chomwechopano, akulozera mmbuyo kwa Danieli. Mateyu 24:15, kwa inuamene muli kuzilemba. Ine ndikufuna inu, mmodzi aliyensetsopano, makamaka usikuuno ndi—ndi Lamlungu lotsatira,mukabweretse mapensulo amenewo ndi mapepala, chifukwaife tiri…kupatula ngati muli nayo tepi. 24, ndi ndime ya 15,“Ndipo pamene chotero…”

Ndipo pamene inu choteromudzawona chonyansa chakupululutsa, chonenedwa ndi Danieli mneneri,…Taganizani! Izi ndi foro handiredi eyite filii, -zinai, -zisanu,

zaka eyite sikisi nthawi isanafike. Zaka foro handiredi eyitesikisi nthawi isanafike.

…Daniele mneneri, ataimirira mu maloopatulika,…Tsopano yang’ananimuBaibulo lanu. Izi ziri mokutidwa.…(yense yemwe awerenga, msiyeni iye amvetse:)

110 Tsopano, Iye akuyankhula kwa Ayuda. Iwo akufuna kutiadziwe, “Nanga bwanji kachisi uyu? Ndi liti pamene iye atiadzawonongedwe? Ndi liti pamene iye ati adzamangidwenso?Ndi liti pamene pati padzafike nthawi imene sipadzakhalamwala umodzi pa umzake?Kodi izo zidzathamotalika bwanji?”111 Iye anati, “Pamene inu mudzawona ‘themberero lopangachipululutso, chitaima pamene…’ Daniele, ‘anaima mu malo

Page 30: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

30 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

opatulika.’” Anati, “Pamene inu mudzawona izi zikufikapochitika, tsopano msiyeni iye amene awerenga amvetsechimene iye akuchikamba.”

Ndicho chifukwa ife tiri kupemphera kwa Mulungu,kuti apange izo mwangwiro kwambiri, kuti pasakhalemthunzi umodzi wa chikaiko. Chifukwa, ife sitimayenerakuika kutanthauzira kwathukwathu kwa zinthu zimenezo.Izo ziyenera kubwera kupyolera mu PAKUTI ATEROAMBUYE. Chotero, ine ndikuzisiyira izo pomwepo mpaka inenditazimvetsa.

Anaulula zinthu zonse kwa iye, “themberero” lija.112 Ndipo, kumbukirani, ilo liri nalo tanthauzo la pawiri, mongangati, “Ndidzaitana mwana wanga kuchokera mu Igupto.”Monga Israeli anaitanidwako; chomwechonso Yesu, MwanaWake, anaitanidwako.

Ndipo zimenezo zidzakhala ziri chimodzimodzi basi, moonamonga ine ndiri kuima pano. Ndipo Iye anazichita izo mwakuti,ndipo Iye wazipanga izo zonse kubisika, zonse zabisika kwaMpingo. O, pamene ife titafike ku zimenezo, kufika mukufutukuka pasanu ndi kamodzi kwa kumvetsa kumeneko,momwe Iye wakhala atazibisira zonse izi kwa Mpingo; koterokuti Mpingo ukanakhala uli kupenyerera izo miniti iliyonse,sunali kudziwa liti Iye anali kudza. Koma tsopano m’badwowa Mpingo uli pafupi kutha, kotero zangokhala zokonzekeratsopano Kudzako, basi uli kungokonzekera.113 Awa ali amodzi a Malemba ofunika kwambiri mu Bukhu.Kodi iwo amachita chiyani? Iwo amatiwuza kutsekera kwafuko la Ayuda, anthu Achiyuda. Lemba ili, makumi asanu ndiawiri a masabata, ilo limaulula ndi kutiwuza chimodzimodzikuyambira pa nthawi imene Daniele anayambira kumeneko,mpaka mapeto a chimaliziro. Ndicho chimodzi cha zidutswazosunga nthawi zopambana. Ndi angati anandimva ine ndikuti,“Ngati iwe ukufuna kuti udziwe tsiku lanji la sabata limeneliri, yang’ana pa kalendara. Ngati iwe ukufuna kuti udziwenthawi yomwe ife tiri kukhalamo, yang’ana Ayuda”? Ndikokulondola. Iyo ndiyo kalendara ya Mulungu, ikutengedwakuchokera momwemu umu.Wazamulungu aliyense, wophunziraBaibulo aliyense, aliyense, angati akuuzeni inu kuti ichi ndichochidutswa chodziwira nthawi, Ayuda.

Tsopano kodi ife tiri ndi nthawi yanji? Ndife basi…anthu,kwatentha, o, ine…114 Izo ziribe kanthu koti zichite nawo Amitundu; ZisindikizoZisanu ndi ziwiri izi, Miliri Isanu ndi iwiri, Matsoka Asanu ndiawiri, Malipenga Asanu ndi awiri, alibe chinthu chimodzi chotizichite. Mpingo wa Amitundu udzakhala uli mu UIemerero panthawi imeneyo. Ziribe kanthu koti zichite nafe ife, Mpingo wa

Page 31: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 31

Amitundu. Izo zikuchita kokha ndi Israeli. “Daniele, anthu akondi Yerusalemu.”115 Tsopano, ndipo akuwulula zoona zakuti Mulungu amachitanawo kokha Ayuda pamene iwo ali mu dziko la kwawo. Aleluya!Apo ndi pamene ine ndikuganiza zinakhudza pachimake, apopomwe.

Iwo nthawizonse akuyesa kuti azilola kuchokera pa nthawiimene Israeli anali kumeneko pa nthawi ya Daniele. Ndipowolemba wina wamkulu…Chifukwa, ine ndikudziwa enaomutsatira ake akhala pomwe pano, ine sindizinena izo. Komandicho chifukwa iwo anali nazo zinthu zonse zabodza izi.116 Kodi inu mukudziwa momwe achi Millerite, iwo asanakhalea Seventh-day Adventists, chimene iwo anachita kumtundakuno? Mu 1919, anatenga mapiko awo, (inu nonse munaziwonaizo mu pepala ya Courier), ndipo anakwera pamwamba kunokuti akawuluke kumapita, mmawa umenewo. Kumene kujakunali kutenga makumi asanu ndi awiri a masabata a Daniele.U—nhu, achi Millerite. Ndiye, kenako, ndi Akazi a EllenWhite, yemwe anali mneneri wawo wamkazi, anatembenukaapo nadzitcha okha Seventh-day Adventists. Ndipo tsopano iwoasintha dzina lawo kukhala Liwu la Uneneri. Mwaona? Mainaatatu osiyana a chipembedzo chomwecho.117 Tsopano, koma iwo anali kulakwitsa, chifukwa iwo analikuyesa kuti aziyika masabata makumi asanu ndi awiri amenewokwa Ayuda ndi Amitundu omwe. Ndipo Iye akuti apa, “Ndi zakwa anthu ako.” NdipoMulungu sanachitepo konse nawo Ayudakunja kwa Palestina. Ndipo pamene Mesiya, pa makumi asanundi awiri, ndi masabata awiri, analikhidwa, (osati chifukwa chaIyemwini; chifukwa cha ife, anadulidwa), Israeli anamwazikana,ndipo sanali (nkomwe) sanabwerere ku dziko la kwawokufikira zaka zingapo chabe zathazi. Chotero, nthawi siinalikuwerengedwera mkati mmenemo kwa m’badwo wa Mpingo.Kodi inumukuzimvetsa izi? [Osonkhana, “Ameni.”—Mkonzi.]

Sizikanati zikhale 1919. Ine ndikhoza kusonyeza chinachakechinachitika mu 1919, koma ndi pamene Mngelo uja, uthengawa Mngelo wachitatu unakantha ndipo Tsoka linapita.Chimodzimodzi. Koma sizinali…Apo panali pamene nkhondoinayima mwa njira yachinsinsi. Ife tizipeza izo mu mutu wa 7pamene ife tidzafika ku izo, pamene ife tidzafika ku mutu wa7. Inu nonse mwandimva ine ndikulalikira zimenezo, nthawizambiri, mwaona, pamene uthenga wa Mngelo unati, “Gwiramphepo zinai za dziko lapansi mpaka ife titawasindikiza Ayuda,antchito.” Ndipo, tsopano, iwo anali akudikira mpaka m’badwowa Amitundu wonse utachokapo.

Ndiye pamene Iye anabwera umo, ndiye—ndiye Iyeakuwasindikiza Ayuda, handiredi forte foro sauzandeakulandira Mzimu Woyera. Apo pali handiredi forte

Page 32: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

32 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

foro sauzande, atasindikizidwa. Chivumbulutso 7. Inumwawerengapo izo.

“Ndipo ine ndinawona chiwerengero chachikulu chiri kaleKumwamba,” Yohane anawaona, “a mitundu yonse, malirime,ndi fuko, ndipo iwo anaima pamaso pa Mulungu, ali ndikanjedza mu manja awo, ndipo atavala miinjiro yoyera,akuimba. ‘Aleluya! Ameni! Ulemerero, nzeru, ulemu, ukulu,mphamvu, zikhale kwa Mulungu wathu kwa nthawi za nthawi.Ameni!’ iwo akufuula.”118 Yohane sankakhoza kuzimvetsa pamenepo. Koma iyeanayang’ana mmbuyo ndipo iye anawona pa Phiri la Sinai,(ulemerero) handiredi forte foro sauzande omwe analiasanaipitsidwe ndi akazi. Ayuda! Akazi, mipingo! Iwo analiasanajowinemabungwe, Achilutera, Chimethodisti, Chibaptisti,ndi Chipresbateria. Koma iwo anali ali Ayuda kuchokeraku chiyambi, Orthodox, ndipo iwo anali naye kachisi wawokumeneko, akupembedza pa Phiri la Sinai. Ndiwo handirediforte foro sauzande. Ndipo zitatha izi; Mpingo uli kale muUlemerero. Mwaona?119 Kotero, Bambo Smith anali kulakwitsa, anayenera kukhalaali. Chifukwa, iwe ungaziyike motani izo apa mu 1919, kutengahandiredi forte foro sauzande? Ndiye kuti wabwereranso mu chiRussellite kachiwiri. Mwaona? Ndiye kuti iwe wabwereranso kuchiphunzitso chachi Russellite, kuti, “Yesu anabwera mu 1914.1919 Iye anawutenga Mpingo Wake. Ndipo tsopano Iye ali thupilachinsinsi likuyenda ponseponse pa dziko lapansi, kuwuka…kupita ku manda a agogo aakazi ndi manda a agogo aamuna,ndi kuwawukitsa iwo onse, iwo onse amene anali achi Russelite.”Zamkhutu! Izo sizikupanga chanzeru mu Mawu. Izo sizingatizituluke molondola. Ayi, bwana. Izo sizitero.120 Koma, Mulungu ali nacho Choonadi. Ndipo Mulunguali Mmodzi Yemwe angakhoze kuwulula Icho ndi kuchiikaIcho mmenemo, ndi kusonyeza Icho chimodzimodzi, kwaife. Mwaona? Ine ndikukhulupirira Iye adzachita izo. Inesindiri kudziwa izo. Ine ndikukuuzani inu Choonadi. Inesindiri kuzidziwa, koma ine ndiri kukhulupirira. Ine ndirikukhulupirira kuti Iye atero.121 Kotero, inu mukuona, Mulungu samachita nawo konseAyuda. (Ine ndikufuna inu musunge izi mu malingaliro)malingana ngati Israeli…122 Ndipo pamene ine ndimayesa kumuuza m’bale uyu wakhalacha apa, yemwe akukamba za kupita ku Israeli, khalani kutalindi Israeli! Khalani kutali kwa iye, anthu nonse inu amenemukukamba zowatembenuza Ayuda. Uthenga uwu usanathe,inu mudzawona kuti ndi PAKUTI ATERO AMBUYE, mwaMawu ndi mwa Mzimu. Israeli adzatembenukanso, fuko lonse,mu usiku umodzi. Baibulo linanena chomwecho. Koma Uthenga

Page 33: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 33

suli konse kwa iwo. Ziripo zigawenga pang’ono zomwe zirikunja, ndi zina zotero monga izo, zimene zikubwera umu, ndikokunja kwa thupi lenileni la Ayuda, amene ati abwere umu ndikukhoza kupulumutsidwa. Ndizo zoona. Ine ndikukhulupirirazimenezo ndi wanga wonse—mtima wanga.

Koma, kumbukirani, malingana ngati Israeli ali kunjakwa fuko lawo, iwo sangakhoze kupulumutsidwa. Tsopanoiwo akubwerera. Ndipo iwo adzapulumutsidwa, fuko lonselathunthu, mu tsiku limodzi. Baibulo linanena chomwecho.Tsiku limodzi; adzabweretsa, kwathunthu, Israeli yensekubwerera kwa Mulungu komwe. Uko kudzakhala kuli chinthuchamphamvu chotero chomwe chiti chidzagunde Israeli limodzila masiku amenewa, mpaka kuti icho chidzagwedeza fuko lonse.Ngakhale mneneri anafuulira, ndipo anati, “Mu tsiku limodziinu mwachichita ichi.” Mu tsiku limodzi, iwo adzachiwona Icho.Uko kudzakhala chinthu champhamvu.123 Lingaliro langa, iye adzakhala ali mneneri wamphamvuyemwe ati adzawuke ndi kudzaima pamaso pa Israeli, ndikutsimikizira kwa iwo kuti Mesiya akadali wamoyo. Mesiya ujayemwe iwo anamukana…?…124 Iwo akuwerenga Baibulo laling’ono lija tsopano, Baibulola Israeli. Iwo amawerenga Ilo kuyambira mmbuyo kumkakutsogolo, momwe iwo amawerengera Ilo. Ndipo inumukudziwamomwe chinenero cha Chiyuda chimalembedwera. Ndipo koteropamene Iwo akuwerenga Ilo…Ndipo iwo akuwerenga lomweLewi Penthrus uja anatumiza kwa iwo, Mabaibulo milioni.Iwo anati, “Ngati Yesu uyu…” Amenewo anali Ayuda ajaamene anabweretsedwa kuchokera uko ku Iran, ndi mpakakumeneko, sanayambe amvapo za chinthu chotero chongaMesiya. Ndipo pamene iwo anakonzekera kuti abwerere kudziko la kwawo, bwanji, iwo sakanati alole kuti akwere pandege zimenezo. Iwo anali akulimabe ndi makasu akale. Inumunawerenge izo mu magazini ya Look. Ndi angati anawerengankhani zimenezo mu Look ndi Times mag-…? Bwanji, zediinu munatero. Mwaona? Iwo sakanati alole kukwera mmenemo.Mphunzitsi wachikulire uja anaima panja kumeneko ndipoanati, “Kumbukirani, mneneri wathu anati ife tikanadzapitapobwerera ku dziko la kwathu pamapiko amphungu.”Aleluya!

Mafuko akusweka, Israeli akuwuka,Zizindikiro zomwe Baibulo linaneneratu;Masiku a Amitundu akwanira, ndi zowopsyazachuluka;

“Bwererani, O omwazika, kwanu.”125 Inu kulibwino kuti muziwuka. Inu mwazimva izo ndikuzimva izo, ndi kuzimva izo, koma iyo idzakhala ili nthawiyotsiriza, limodzi la masiku amenewa. Israeli akubwerera kudziko la kwawo. Tsiku limene Mulungu watsimikizira Israeli

Page 34: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

34 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

kuti akhale fuko, ndilo tsiku limene sipadzakhala Wamitunduwina kupulumutsidwa.126 Ine nditsimikizira izo mwa makumi asanu ndi awiri amasabata awa, ngati ine ndingakhoze kokha kuwapeza masikuamenewo. Ine ndikupita uko ku…kuti ndikatengemakalendaraa akasidi, ndi—ndi ya Julian, ya akasidi, ndi ya Chiroma, ndi onsea iwo. Alipo ena owonjezera, penapake. Chiripo chinachake.Mulungu akudziwa za zimenezo, ndipo, Iye—Iye ali wokhozakuti aziwulule izo. Mwaona? Ine ndikudziwa kalendara yaJulian ili nawo filii wandiredi sikisite faifi ndi kotala ya tsiku,mu chaka. Kotero, o, iwo onse ali osokonezeka, koma chiripochoonadi, penapake.127 Ine ndikuwona mipingo yochuluka kwambiri, mabungweochuluka kwambiri, anthu ochuluka kwambiri akutsatiraichi, ndipo ena, “Tikuoneni Maria,” ndipo ena akupembedzaichi, ndi chija, chimzake. Payenera kuti pakhale Choonadi,penapake. Payenera kukhala pali Mulungu, penapake. Payenerakukhala pali Uthenga, penapake. Ine ndikuwona aneneri abodzaakuwuka, akuchitamonga kuzindikira zammitima, ndimitunduyonse ya zinthu ziri kuchitika. Ndiye, payenera kukhala palimmodzi weniweni kumeneko, penapake, kumene chokoperachochapangidwa kuchokerako.128 Ine ndimawawona anthu akulowa mu thupi, ndi kumafuula,ndi kumapitiriza, ndi kutuluka panja ndi kumakhalamitundu yonse ya moyo. Payenera kukhala pali MzimuWoyera weniweni uko, penapake. Ine ndimawawona anthuakuchita mwachipembedzo, ndi zina zotero, ndi kumayesakukhala auzimu. Ine ndikudziwa alipo Mulungu weniweni,penapake. Ulipo Mzimu weniweni, penapake, chifukwa uyo ndiwachinyengo wakale yemwe wapangidwa kuchokerako, mmodziwakale wokoperayo. Payenera kuti pakhale chinachake chimenechiri chenicheni: mwamuna, anthu, Mpingo, Mulungu. Payenerakuti pakhale chinachake choona, penapake, chifukwa izizangokhala zokopera kuchokera kwa icho. Chiripo chinachakechenicheni, penapake.129 Ine ndinanena kwa mpingo uno, zokhudza mphatsozanu. [M’bale Branham akugogoda pa guwa kanai—Mkonzi.]Mvetserani kwa mphatso zanu; ziyikeni izo mu Baibulo. Musatimutenge zoloweza mmalo, pamene mlengalenga muli modzazandi zenizenizo. Tiyeni tisunge zenizenizo. Tiyeni titenge zenizenikapena tisakhale ndi chirichonse nkomwe. Ameni.130 Tsopano, kutseka, ndi choona kuti Mulungu amachitanaye Israeli kokha pamene iye ali mu dziko lakwawo. Tiyenititenge pamene Mulungu…Abrahamu anachoka ku dzikola kwawo ndipo anapita nakalowa mu Igupto, nchiyanichinachitika? Iye anayenda mochoka ku chifuniro cha Mulungu,ndipo sanadalitsidwe nkomwe mpaka iye atabwerera ku

Page 35: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 35

dziko la kwawo. Mulungu sanachite naye konse iye, panalibemasomphenya amodzi, wopanda kanthu kalikonse, mpaka iyeatabwerera ku dziko la kwawo.131 Tayang’anani pa Israeli pamene iwo anali atatumizidwa ukomu Igupto, zaka mazana anai. Wopanda chozizwitsa chimodzi,opanda chizindikiro chimodzi, opanda chinthu chimodzichimene chinachitika pakati pawo, palibe zinalembedwamu mbiriyakale ya Bukhu. Okalamba omwewo a naintenaini; ankapita ku mpingo, kupereka mwanawankhosa,kunena “Tikuoneni Maria,” kapena chirichonse chimenechinali, kubwerera mmbuyo. Chaka chotsatira, njira yomweyo.Ansembe onse ankatsutsana, “Mphunzitsi Wakuti-ndi-wakuti!Ife tisankha Mphunzitsi Wakuti-ndi-wakuti. Iye ali nawomaphunziro abwinoko. Iye amadziwa bwino za Aigupto.”Chinthu choyamba inu mukudziwa, Aigupto ndi—ndi onse aiwo, anali chinthu chofanana.132 Ndicho chinthu chomwecho chimene chachitika kwampingo. Ife tonse tapita kuti tikakhale Amethodisti, kapenaAbaptisti, kapena Apresbateria. “Ndipo ife tapeza digiriikuchokera ku Hartford! Ife tiri nayo digirii kuchokera kuWheaton! Ife tiri nayo digirii yochokera kwinakwake, kapenaBob Jones! Ife, ife tiri nayo Bachelor ya Luso! Ife tiri nayo D.D.,LL.D., kapena chinachake chimzake!” Kodi izo zawonkhetseraku chiyani? Mulu wa zamkutu.

Ndi momwe izo zinaliri mu Igupto. Ndipo Mulungusanachite naye konse Israeli mpaka iye atabwerera ku dziko lakwawo.133 Ndimveni ine! PAKUTI ATERO AMBUYE, Mulungusadzachita nawo Mpingo Wake mpaka Iwo utabwerera kudziko la kwawo, Uthenga wa orali. Kubwerera ku chiyambi!Chokani ku malingaliro anu a Chimethodisti, a Chibaptisti, aChipresbateria; zanu za Chipentekoste, Assemblies, Aumodzi,Autatu, ndi Akasanu, chirichonse chimene chiri; mpingo waMulungu, Nazerini, Pilgrim Holiness, mpingo wa Khristu, konsekayendetsedwe ka wotsutsakhristu! Ndipo ine ndikuzindikirachinthu ichi chikukantha dziko. Zonse zolakwika; zonse zaMdierekezi. O, mai! Alipo amuna aumulungu mu chirichonsecha izo. Alipo anthu aumulungu mu chimodzi chirichonsecha kayendetsedwe kameneko. Koma bungwe, mwa ilolokha,si la Mulungu, ndipo Mulungu sadzalidalitsa konse ilo. Iyesanayambe wachitapo izo.134 Ine ndikumufunsa wazambiriyakale aliyense (inu amenemuti mudzamvere tepi iyi) kuti mudzalembe ndi kundiuzaine pena pamene, mpingo unachita bungwe, ngati Mulungusanauyike iwo pa alumali ndipo sanadzachite konse nawo iwokenanso. Ndiwuzeni ine pamene Iye anayamba wawukitsaChilutera kachiwiri, Wesile ndi Chimethodisti, kapena

Page 36: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

36 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

Chipentekoste. Sanachitepo nkomwe! Bungwe limenelolinagona pamenepo, ndipo linawuma ndipo nlovunda! Mulunguanatenga anthu pawokha ndi kuyesa kuwalozera anthu kutiabwerere ku dziko lakwawo. Ndiyeno, anthu pawokha ofookachotero ndi achikazi, ndi mtundu wina wa digirii, mpaka iwoanachita bungwe lina, ndi kulipanga ilo mwana pawiri wagehena kwambiri kuposa zomwe izo zinali pa kuyamba nazo.135 Koma, penapake, zedi, Yehova ali naye munthu yemwe Iyeangaike manja Ake pamenepo, yemwe sati adzanyengerere ndiiwo…-waumulungu, bungwe lopanda umulungu; yemwe atiadzawatembenuzire anthu kubwerera ku Thanthwe, KhristuYesu, kubwerera ku pentekoste yapachiyambi ndi MzimuWoyera wapachiyambi, wa zizindikiro zapachiyambi ndizodabwitsa zapachiyambi. Ndithudi Iye ali naye mmodzi,penapake, yemwe sadzasweka pansi pa mtundu uliwonsewa kusautsidwa, kuthawa, kusiyitsa, kugwera kunja, chinachirichonse; yemwe ati adzakhalebe nacho icho.

Mulungu samadalitsa konse Israeli mpaka iye atafika kudziko lakwawo.136 Mulungu sadzakudalitsani konse inu, Amethodisti,Abaptisti, Apresbateria, Akatolika, kapena a Pilgrim Holiness,Anazerini, a mpingo wa Khristu, kapena—kapena bungwela Chipentekoste. Iye sadzakudalitsani konse inu mwanjiraimeneyo. Bwererani ku dziko lakwanu, ku chiyambi, kubwereraku chochitika cha chipentekoste monga izo zinachitikira paTsiku la Pentekoste pamene Mphamvu ya Mulungu wamoyoinasintha zikwi zija za anthu, ndi kuyika mtima wawo poyakandi Moto wa Mulungu, chimene chinasonyeza chenicheni;osati zizindikiro zosanzira, osati zowerenga malingaliro zinazongopangidwa, osati zotonza zina, ndi kulowa mu mjahawa makoswe monga ife tiri nazo mu Amerika. “Ndani yemweangakhale nayo hema yokulitsitsa?” Kapena, “Ndani angakhozekukhala nawo unyinji wokulitsitsa?” Ndi kusiyana kwanjikumene izo zimapanga kwa Mulungu? Mulungu akufunaanthu owona mu mtima, osati unyinji waukulu. Ndipo ifetonse tiri nawo mjaha wa makoswe kuno, ukuthamangidwa.Ndi chamanyazi bwanji, kuti tiwone ngati ife tingakhozekuwonjezera chikwi china ku bungwe lathu. Ndi chamanyazi.Iye akufuna ife tibwerere ku Choonadi, kubwerera kuMzimu, kubwerera ku Kuwala kolondola, kubwerera kumsewuwawukulu mwa Khristu, kubwerera ku Choonadi. Iyeangakhoze bwanji kutidalitsa ife konse momwe ife timachitira?Iye sangatero.137 Iye sanadalitse konse Israeli mpaka iwo atabwerera kudziko lolonjezedwa. Ndipo pamene iwo anabwerera mu dzikololonjezedwa, zizindikiro ndi zodabwitsa zinayamba kuchitika.Iye anatumiza munthu mpaka uko pakati pawo, dzina lakeMose. Kodi Mose uyu anabwera uko ndi chiyani, zamulungu

Page 37: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 37

zopukutidwa? Kodi iye anabwera uko ndi digirii ya Bachelor yaLuso?Kodi iye anabwera uko ndi LL.D., Ph.D.? Iye anabwera ukondi mphamvu ya Yehova, ndi uthenga, “Bwererani, kuchokeramu dziko lino, kupita ku dziko la kwanu. Bwererani, Oomwazika, kupita kwanu.” Ameni!138 Kwa pafupifupi zaka zikwi ziwiri, Ayuda akhala ali ukoku dziko la kwawo, anamwazikana ku mphepo zinai zadziko lapansi. Momwe ife tingakhoze kuwupangira Uthengauwu kutha kwa masabata tsopano, ngati ife tikanati tipitemwatsatanetsatane. Ife tikhoza kumutsatira Israeli kumbuyokomwe ndi kusonyeza pamene iye anamwazidwa ndi Ufumuwa Roma, pa kumukana kwawo kwa Mesiya; momwe iyewawongoleredwera ku fuko lirilonse la pansi paKumwamba.

Kupita kubwerera kwa Yakobo, Israeli, kubwerera muGenesis 44 ndi 45, ndi kusonyeza kumbuyo uko momweiye anazidalitsira mbadwa zimenezo ndi kuwawuza iwochimodzimodzi pamene kuima kwawo kuti kudzakhale mumasiku otsiriza. Ndipo ine ndikhoza kulozera kwa inuchimodzimodzi (fuko lirilonse) la Israeli, fuko lirilonse laIsraeli, likuima chimodzimodzi mu mafuko kumene iwo akanatiadzakhale ali. Ndipo pano ife tiri lero.139 Myuda yemwe ife tikumudziwa, ameneyo si Myudaweniweni. Myuda weniweni ndi uja wa Chiorthodox weniweniyemwe sanadziyipitse iyeyekha ndi zinthu za mdziko, yemwesanapite kunja ndi kukajowina mipingo ina. Ndiwo ameneali kubwerera kutsidya, akukhala moyo pa tchizi ndi mkate,kumtundako cha mmbali za mapiri, osaloledwa mu mzindawakalewo. Anachita kuwamangira iwo mzinda ku mbali iyi, mudziko lopanda mwini, ali nayo mifuti yamakina atalozetsa mbalizonse. Koma iye wayamba kuphukira mphukira zake. Ameni,ndi ameni! Nthawi ili pafupi.140 Kumeneko kuli Aishmaeli ndi Isaki, kuyima kumeneko,akukangana zokhudza dzikolo, panobe, koma ilo ndi la Israeli.Ngati inu mutadzapezeka kuti mwapita mu Yerusalemuwatsopano, iwo sadzakulolani inu kuti mubwere ku Yerusalemuwakale. Iwe umayenera kupita kumeneko poyamba ndikuwalola iwo kuti akufotokozere izo zonse iwe, Aluya,ndiye nkukutengera iwe kupita ku mbali inayo. Iwo ndiana Aishmaeli. Koma, dikirani, pali kubwera nthawi yomweana a Mulungu ati adzawutengenso iwo. Ndiko kulondola.Yerusalemu adzamangidwanso kachiwiri. Nsembe ya patsikuidzayikidwanso.

Ndipo wotsutsakhristu adzapanga pangano la masabataasanu ndi awiri otsiriza awo. Ndipomkati mwa iwo, iye adzaswapangano limenelo, kuwatembenuzira iwo onse ku Chikatolika.Themberero lidzafalikira pa chinthu chonsecho, monga choncho,ndiyeno mapeto adzakhala ali.

Page 38: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

38 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

141 Penyani, “makumi asanu ndi awiri a masabata.” Eya, iwoali pafupi zaka zikwi ziwiri zomwe iwo akhala atachokako.Iwo akhala atathamangitsidwako tsopano. Iwo ndi anthumonga izo zinali mu kuwumitsidwa mtima kwa Farao. Iyeanachita kuwuumitsa mtima wa Hitler. Mamilioni a iwoanafa. Tayang’anani pa Eichmann uyu, wolakwa pa kuphaAyuda mamilioni asanu ndi imodzi. Mamilioni asanu ndiimodzi a iwo, miyoyo ya anthu, makanda, ana, akulu, onsekuikidwa ku imfa; Eichmann, munthu mmodzi. Tayang’ananipa Russia, momwe inu munawathamangitsira iwo kupitauko. Iwo anawathamangitsira iwo kulikonse. Iwo akhala fukolonyozedwa.142 Koma chifukwa cha chikondi cha ndalama chawo,iwo ali kubwereranso kachiwiri. Koma ochepa apang’onoawo akubwerera ku Palestina. Ameni, abale! Pamene inumukumuwona iye akuyamba kubwera ku dziko la kwawo!143 Iwo ali nawo okwanira kumeneko tsopano oti akwanitsehandiredi forte foro sauzande. Ndi chiyani chikuchitika? Iwoadzamudziwa Yosefe wawo. Inu musati mudandaule. Inde,bwana. Ndipo iwo onse ayima kumeneko kuyembekezera kutiizo zichitike. Ndi ora ilo lomwe…144 Mafuko awatcha iwo fuko, chaka chatha chomwechi.Pamene icho chigunda, ife tiri pafupi ndi mapeto, Mpingo waAmitundu wapita. Kotero, pafupifupi nthawi iliyonse, Mulunguakhoza kuti, “Israeli ndiwo anthu Anga.” Pamene izo zichitika,Amitundu atsirizidwa.145 “Iwo adzapondereza,” anatero Yesu, mu Mateyu 24.“Themberero lopangitsa bwinja, iwo adzapondereza makomaa Yerusalemu kufikira nyengo ya Amitundu ikhale itatha.”Pamene iyo yatha, ndiye Ayuda adzabwereranso kukalowa muYerusalemu, kuti akakhazikitsenso kachisi ndi kupembedzakwa mkachisi. Ife tizipeza zonse izi muMauthenga otsatira awa,makumi asanu ndi awiri a masabata a cholinga chofutukukapasanu ndi kamodzi.

Tsopano ine ndiwerenga izo ine ndisanafike potseka,chifukwa ikhala ili pafupi kukwana nthawi pamenepo kuti ifetizipita kunyumba, ndiye mukabwererenso usikuuno pa sevenikoloko.146 Choyamba, choyamba, ngati inu mukulemba izo, “Kutiatsirizitse cholakwira.” Daniele, mutu wa 9, ndime ya 24.“Kuti atsirizitse cholakwira,” choyamba. “Kuti apange kuthakwa tchimo,” chachiwiri. “Kuti apange chiyanjanitso chakusaweruzika,” chachitatu. “Kuti abweretsemo chilungamochosatha,” chachinai. “Kuti asindikize masomphenya ndiuneneri,” chachisanu. “Kuti adzoze Wopatulikitsa,” chachisanundi chimodzi. Ndipo ndi zomwe ife titi tiyankhulepo usikuuno.Mulungu, kubweretsa poti zikwaniritsidwe!

Page 39: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 39

147 Tsopano dikirani, tiyeni ife tidutse pa izo kachiwiri,kotero kuti inu muzimvetse izo. Choyamba, “kutsirizitsacholakwira.” Chachiwiri, “kupanga kuthetsa kwa tchimo.”Chachitatu, “kupanga chiyanjanitso cha kusaweruzika.”Chachinai, “kubweretsamo chirungamo chosatha.” Chachisanu,“kusindikiza masomphenya ndi uneneri.” Chachisanu ndichimodzi, “kudzoza Wopatulikitsa.”

Ndiroleni ine ndiwerenge izo kwa inu tsopano, kuchokera—kuchokera mu Baibulo. Ndi ndime ya 24.

Asanu ndi awiri-…masabata atsimikizidwira paanthu ako (Ayuda) ndi pa wako wopatulika—pamzindawako wopatulika (Israeli, Ayuda, Yerusalemu), kutiatsirizitse…zolakwira (choyamba),…kuti apangekutha kwa tchimo, (chachiwiri),…kuti apangechiyanjanitso cha kusaweruzika (chachitatu),…kutiabweretsemo chilungamo chosatha (chachinai), ndi kutiasindikize masomphenya (chachisanu)—masomphenyandi uneneri, ndi kuti adzoze Opatulikitsa (chachisanundi chimodzi).

148 Ndizo chimodzimodzi zomwe Iye anabwera kuti adzamuuzeiye, zomwe zikanati zidzachitike, ndiyeno mapeto akanatiakhalepo.149 Tsopano, usikuuno ife titenga chomwe zinthu zimenezo ziri,ndi kuwona momwe ife tayandikirira ku zimenezo. NdiyenoLamlungu lotsatira, kubweretsa umo ndi kuziyika zochitikamu nthawi izi chimodzimodzi pamene ife tiri kuima. Inendikumukonda Iye.150 Israeli akubwerera ku dziko lakwawo, Israeli. Ndiroleniine ndingonena izi tsopano pamene…Ine ndikuganiza izisiziri pa tepi. Ndiroleni ine ndinene izi. Ora lomwe limeneIsraeli akukhala fuko…Chifukwa chimene ine nthawizonsendakhulupirira, pamaso pa kalasi yanga pano, kuti panalichinachake chimene ine ndikanati ndikhale nalo gawo, inendisanafe, la kumutengera Israeli kubwerera kwa Ambuye.Chifukwa, pamene ora lomwe, la chikalata cha Pan American,limene Israeli anatchedwa fuko, kwa nthawi yoyamba munthawi ya zaka zikwi ziwiri kuchokera chimwazikireni chawo,osati anthu; zinali pa ora lomwelo, chimodzimodzi ku ora,limene Mngelo wa Ambuye anakomana nane kutsidya kujandipo ananditumiza ine ku…ndiUthenga. Chinthu chomwechokumene. Mei 7, 1946.151 Tsopano, ndiye, chinthu china chimene chimandipatsa inekuti ndidziwe. Ndicho “kubwezeretsa mitima ya ana kubwererakwa atate, ndi mitima ya atate kwa ana,” Uthenga. Zindikirani,Malaki 4 (osati 3), 4!152 Chinthu china. Pamene Billy, mwana wanga, ndi ine, M’baleErn Baxter, tinali pa ulendo wathu wopita ku Palestina, ife

Page 40: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

40 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

titatha kukomana nawo Ayuda kwa M’bale Arganbright, ndipoiwo anawuona msonkhano. Lewi Penthrus anali atawatumizaMabaibulo awa kumeneko. Ndipo iye anati…Ayuda awaanabwera, anati, “Ngati inu muti muitanitse gulu la atsogoleria Israeli, ine ndikutanthauza, osati a rabbi atsopano awandi maphwando awo onse, koma kuitana atsogoleri enienia Chisraeli palimodzi. Ndipo ife tawerenga ChipanganoChatsopano ichi, ndipo ife tikudziwa kuti pamene Mesiyaabwera, Iye adzatiuza ife zinthu zimenezi, monga mkazi wakuSamaria. Ife tikudziwa kuti Mose anati Mesiya wathu akanatiadzakhale mneneri. Ndipo pamene inu mungakhoze kuwauzaiwo ndi kuwasonyeza iwo, mwa Lemba,” limene ife titi tilowemomu Uthenga wa usikuuno, “kuti iwo ayenera kuti achititsidwechidima ndi mitima yawo kudulidwa, kuti danga la Amitundulikakhoze kubwera, kuti ife tikakhoze kukhala nayo nthawi yachiyanjanitso kwa Amitundu. Ndipo mitima yawo inaumitsidwachimodzimodzi basi monga izo zinali mu nthawi ya Yosefe, ndizina zotero. Ndiyeno nkuwabweretsa Ayuda amenewo pa malo,ndi kuwaitana amuna amenewo kuchokera kwa omvera, mongamomwe inumukuchita nawoAmitundu awa pano, mwa kudzozakumeneko kwaMzimu.” Chifukwa, iwo ankati, “Ngati Yesu uyu,ngati Iye ali Mesiya, ndipo mawu anu ali owona, ndiye Iye saliwakufa, ndipo Iye ali wamoyo. Ndipo ngati Iye ali wamoyo,Iye analonjeza kuti adzakhala mwa Ake…wa-…wantchitoWake—antchito, ophunzira Ake. Ndipo ngati ife tingakhozekumuwona Iye akuchita chizindikiro cha mneneri, ndiye ifetikhulupirira kuti Iye ali Mesiya.”

Ndi chinthu changwiro bwanji, kulondola chimodzimodzi.Ndiye, chimenecho chikanati chidzachite chiyani? Fukolikanadzabadwamu tsiku limodzi, pakati pa atsogoleri. Mmodzialiyense wa iwo akanadzati, “Ife tikudziwa izo.” Pamenemphunzitsi ameneyo anena choncho, icho chimakhazikitsa izo.Fuko likanadzabadwa mu tsiku limodzi. Israeli akanadzabadwamu tsiku limodzi.153 Ndipo ine ndinali pa ulendo wanga, ndipo ndinaima kuCairo, Igupto, ndiri nayo tikiti mu dzanja langa, ndipo maminitikhumi ndi asanu kapena makumi awiri aku nthawi yoitana. Iwoanali akukonzekera kuti apange kuitana. Ndipo ine ndinayendapansi kuti ndikawone kachidutswa kakang’ono ka nkalati aka,ndi njovu yaing’ono yopangidwa kuchokera ku nkalati, ndi—mnyanga. Ine ndimati ndikaitumize iyo kwa dokotala mzangawa ine, Dr. Sam Adair, yopsyinjira mapepala. Ndipo ine ndinalikuyang’ana pa iyo. Ndipo Chinachake chinanena kwa ine, “Ilisindiro oralo panobe. Khala kunja kwa Palestina.”154 Kotero ine ndinaganiza, “Uyo ndinali ine chabe ndikuganizazimenezo.” Ndipo ine ndinapitirira.

Chinachake chinati, “Ili si ndiro oralo.”

Page 41: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 41

155 Ndipo ine ndinatuluka kuseri kwa kokonzera ndege.Ine ndinadzutsira mutu wanga kwa Mulungu. Ine ndinati,“Mulungu, kodi ujamunali Inumukuyankhula kwa ine?”

156 Anati, “Ili si ndiro oralo. Khala kunja kwa Palestina. Iyi sinthawiyo.” Ndiye ine ndinatenga tikiti yanga ndipo ndinaisinthaiyo, ndipo ndinapita kuchokera kumeneko mpaka kukadutsaku Roma, ndi kubwerera ku Lisbon, mu Portuguese, ndipokuchokera kumeneko ndinabwerera kuUnited States.

157 Ora linali lisanakwane. Kusaweruzika kwa Amitundusikunadzaze panobe, mpaka pamapeto pa chikho pokha. Komatsiku lina zimenezo zidzakhala ziri, ndipo Mulungu adzatumizawinawake kumeneko yemwe ali mneneri, ndipo adzatsimikizirakwa iwo. Ine ndikudalira kuti Mulungu adzamuwutsa iyenthawi yomweyo, aliyense yemwe iye angati akhale, yemwe atiadzamuwutse iye mwamsanga. Ine ndikukhulupirira kuti izoziyenera kuti zibwere. Ndi chimene ife tikuphunzirira izi, kutiife tiri pafupi zedi.

158 Ndipo, kumbukirani, miniti kumene yomwe Ayudaakulandira Khristu, Mpingo wa Amitundu wapita. NdiyeAmitundu ali nayomiliri ikutsanuliridwira pa iwo, Chisautso.

159 Ndipo—ndipo angakhoze bwanji amuna, alaliki aakulukuphunzitsa, ndi kumayang’ana pa Baibulo ili monga chonchi,ndi kumanena kuti Mpingo udzadutsa mu nthawi ya Chisautso,pamene palibe Lemba mu Baibulo limene limanena zimenezo!Iwo alibe chinthu chimodzi.

160 Munthu anandiuza ine, osati kale litali, anati, “O, MlongoMcPherson amaphunzitsa kuti Mpingo ukanadzadutsa kupyolamu Chisautso, chifukwa ife tidzakhala nyali zowala mu nthawiimeneyo.” Ndi Israeli pamenepo, osati Amitundu.

Amitundu atha kupita kale, Mpingo. Iwo sayenera kutiadutse mu Chisautso ayi. “Chinjoka chinalavula madzikuchokera mkamwa mwake,” mutu wa 17, “ndipo chinapangankhondo ndi otsalira,” namwali wogona. Osati…Mpingoweniweni iwo wapita kale. Iwo uli kale kuMgonero wa Chikwatipa ili, danga la nthawi pomwe Mgonero wa Chikwati utiuzidzachitika, sabata lotsiriza. Ndipo ndi pamene Chisautsochikuyambika, pamene dzombe ndi kusautsidwa kukuwuka pamipingo, zinthu monga zimenezo.

Ndiye, pa mapeto, mu mutu wa 19, pano Iye akubwerandi Mkwati Wake. Aleluya! “Mfumu ya mfumu, ndi Ambuyewa ambuye; chovala choviikidwa mu Magazi, ndipo khamuLakumwamba litakwera pa akavalo oyera, akubwera ndi Iye.Pamenepo Iye akubwera, kuti adzatenge malo Ake a kuZakachikwi. Ameni! O!

Page 42: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

42 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

Dzina lodala, o, Dzina lodala,Dzina lodala la Ambuye;Dzina lodala, o, Dzina lodala,Dzina lodala la Ambuye.Yesu ndi Dzina, Yesu ndi Dzina,Yesu ndi Dzina la Ambuye;Yesu ndi Dzina, o, Yesu ndi Dzina,Yesu ndi Dzina la Ambuye.Kuzani Dzina Lake, o, kuzani Dzina Lake,O, kuzani Dzina la Ambuye;Kuzani Dzina, o, kuzani Dzina,Kuzani Dzina la Ambuye.

161 Inu mumachita motani izo? Inu mumalipanga Ilo kukulamu moyo wanu. Inu mumakhala moyo wotero kuti iwoakhoza kunena, “Uyo ndiye wantchito wa Khristu.” Ndimomwe inu mumalikuzira Dzinalo. Tiyeni tiwone. O, kodi inusimukumukonda Iye? [Osonkhana akuti, “Ameni”—Mkonzi.] O,mai! Nyimbo yathu yaing’ono tsopano:

Mu khola kale lapitalo, ine ndikudziwa zirichoterodi,

Mwana anabadwa kuti adzapulumutse anthuku tchimo.

Yohane anamuwona Iye pa gombe,Mwanawankhosa kwa nthawizonse,

Mwanawankhosa uja amene ali nazo Zisindikizo Zisanu ndiziwiri zija, Mmodzi yekha Kumwamba ndi dziko lapansi analiwokhoza kuti alitenge ilo. Mu kho-…

Mu khola kalelo, ndidziwa ziri choterodi,Mwana anabadwa kudzapulumutsa anthu kutchimo lawo.

Yohane anamuona Iye pa gombe,Mwanawankhosa kwanthawizonse,

O, Dzina lodala la Ambuye.O, Dzina lodala, o, Dzina lodala,Dzina lodala la Ambuye;Dzina lodala, Dzina lodala,Dzina lodala la Ambuye.

162 Ine ndimakonda kupembedza. Si choncho inu? [Osonkhana,“Ameni.”—Mkonzi.] Tsopano, ife sitimabwera ku mpingo kutitidzangomva ulaliki; izo zimamka nawo limodzi. Koma ifetimabwera ku mpingo kuti tidzapembedze, kudzapembedza muMzimu ndi mu Choonadi. Inu mwamva Choonadi; ndiwo Mawu.Mwaona? Tsopano, kupembedza, ndiko kudzifotokoza wekhakwa Iye. Mwaona?

O, Ine Ndimamukonda Mwamuna Uja Wa Ku Galileya!Tipatseni ife poyambira pang’ono pa imeneyo. Inde, bwana.

Page 43: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 43

Inu mukudziwa imeneyo, Teddy? Ine ndaiwala tsopano. Tiyenitiwone. Tiyeni tiwone.

O, ine ndimkonda Mwamuna uja wakuGalileya, waku Galileya,

Poti wandichitira zazikulu.Anandikhululukira machimo onse, nayikaMzimu Woyera mkatimu;

O, ndimkonda, ndimkonda Mwamuna ujawaku Galileya.

Wamsonkho anakapemphera mu kachisi tsikulina,

Analira, “O Ambuye, mundichitire chifundo!”Anakhululukidwa machimo onse, ndipomtendere unayikidwamo;

Iye anati, “Bwerani, mudzawone Mwamunauyu waku Galileya.”

O, ndimkonda Mwamuna uja waku Galileya,waku Galileya,

Poti anandichitira zazikulu.Anandikhululukira machimo onse, nayikaMzimu Woyera mkatimu.

O, ndimkonda, ndimkonda Mwamuna ujawaku Galileya.

Wopunduka anayenda, wosayankhulaanayankhulitsidwa.

Mphamvu ija inayankhulidwa ndi chikondi panyanja.

Wakhungu anapenya, ine ndikudziwazinangokhala

Mphamvu za Mwamuna uja waku Galileya.O, ndimkonda Mwamuna uja waku Galileya,waku Galileya,

Poti anandichitira zazikulu.Anandikhululukira machimo onse, nayikaMzimu Woyera mkatimo.

O, ndimkonda, ndimkonda Mwamuna ujawaku Galileya.

Mvetserani kwa iyi.

Mkazi pa chitsime, anamuuza machimo akeonse,

Amuna asanu anali nawo pa nthawiyo. (NdiIyeyo.)

Anakhululukidwa tchimo lirilonse, ndipomtendere unadza mwakuya;

Page 44: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

44 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

Ndiye anafuula, “Dzawoneni, Mwamuna ujawaku Galileya!”

O, ndimkonda Mwamuna uja waku Galileya,waku Galileya,

Poti anandichitira ine zambiri.Anandikhululukira machimo onse, nayikaMzimu Woyera mkatimu.

O, ndimkonda, ndimkonda Mwamuna ujawaku Galileya.

Ine ndikumukonda Iye. Sichoncho inu? [Osonkhana akuti,“Ameni.”—Mkonzi.] Mtima wanga wonse! Simukutero inu?[“Ameni.”] Kodi Iye si wodabwitsa? [“Ameni.”]

O, wodabwitsa, wodabwitsa, Yesu ali kwa ine,(Iye ali chiyani?)

Wauphungu, Kalonga wa Mtendere, MulunguWamphamvu Iye ali;

O, kundipulumutsa, kundisunga kuchokera kutchimo lonse ndi manyazi,

Wodabwitsa Muomboli wanga, mtame DzinaLake!

Tiyeni tingoweramitsa mitu yathu tsopano ndi kumaganizaza izo.

Ine kamodzi ndinali wotaika, koma tsopanoine ndapezeka, ndine mfulu ku kutsutsika,(mafuko akusweka; ziribe kanthu)

Yesu akupereka ufulu ndi chipulumutsochathunthu;

Iye akundipulumutsa ine, Iye akundisunga inekuchokera ku tchimo lonse ndi manyazi,

Wodabwitsa ali Muomboli wanga, mtameDzina Lake.

O, wodabwitsa, wodabwitsa, Yesu ali kwa ine,Wauphungu, Kalonga wa Mtendere, MulunguWamphamvu Iye ali;

Kundipulumutsa, kundisunga kuchokera kutchimo ndi manyazi,

Wodabwitsa Muomboli wanga, mtame DzinaLake!

O, taganizani za zimenezo!

Kale ine ndinali wotaika, tsopano inendapezeka, ndine mfulu ku kutsutsika,

Yesu amapatsa ufulu ndi chipulumutsochathunthu;

Kundipulumutsa ine, (kodi Iye akuchitachiyani?) kundisunga ine kuchokera ku

Page 45: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 45

tchimo ndi manyazi, (kukwera pamwambapa izo)

O, wodabwitsa ali Muomboli wanga, mtameDzina Lake.

Tsopano palimodzi!O, wodabwitsa, wodabwitsa, Yesu ali kwa ine,Wauphungu, Kalonga wa Mtendere, MulunguWamphamvu Iye;

Bwanji, kundipulumutsa, kundisungakuchokera ku tchimo ndi manyazi,

Wodabwitsa ali Muomboli wanga, mtameDzina Lake.

O, ndimkonda Yesu, (ulemerero!)O, ndimkonda…

Ndine wokondwa ndapulumutsidwa! Ndine wokondwa ndirikuyembekezera Kudza Kwake!

O, ndimkonda Yesu,Chifukwa Iye anayamba kundikonda.

Tsopano ndi manja athu mmwamba, ngati ife tikutanthauzaizo.

Sindidzamusiya Iye,Sindidzamusiya Iye,Sindidzamusiya Iye,Chifukwa Iye anayamba kundikonda.

163 Inu mukumkonda Iye? [Osonkhana akuti, “Inde.”—Mkonzi.]Ndiye inu muyenera kuti muzikondana wina ndi mzake.Chifukwa, ngati inu simuli kuwakonda iwo amene inumungakhoze kuwawona pano, inu mungakhoze bwanjikumukonda Iye Yemwe inu simunamuwonepo? Tiyeni tigwiranechanza wina ndi mzake, tikuti:

O, ndimkonda Yesu,O, ndimkonda Yesu,O, ndimkonda Yesu,Chifukwa Iye anayamba kundikonda.Ine sindidzamu…(Kwezani manja anu kwaIye tsopano. Ndi zimenezotu.)…-siya Iye,

Sindidzamusiya Iye,Sindidzamusiya Iye,Chifukwa Iye anayamba kundikonda.

164 Tangoganizani, Iye anapanga vumbulutso lalikulu lijakudziwika kwa ife. Kodi ife sitiri kumukonda Iye? [Osonkhanaakuti, “Ameni.”—Mkonzi.] Kodi Iye sali wodabwitsa? [“Ameni.”]Ndife othokoza bwanji chifukwa cha Ambuye wathu Yesu;samatisiya ife konse. “Taonani, Ine ndiri ndi inu nthawizonse,ngakhale ku…” Kodi inu akukukomerani Masabata Makumi

Page 46: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

46 MASABATA MAKUMI ASANU NDI AWIRI A DANIELE

Asanu Ndi Awiri A Daniele? [“Ameni.”] O, kodi ife sitirikumukonda Iye? Kodi izo zimachita motani?

Chikhulupiriro changa chikuyang’ana kwaInu,

Mwanawankhosa wa Kalvare,Mpulumutsi…

Zimupembedzani Iye basi, kuchokeramumtimamwanu.Tsopano ndimveni pamene ndikupemphera,Tengerani kutali machimo anga onse,O ndiroleni kuyambira leroNdikhale mwathunthu Wanu!Pamene njira yokhotakhota ya moyo inendiyendamo, (ife tonse timachita zimenezo)

Ndi zokwiyitsa pozungulira ine zifalikira,(Inde, Ambuye.)

Khalani Inu Namulondola wanga;(Ndirondolereni ine kupyola mu izo,Ambuye.)

O thamangitsani mdima usanduke usana,Pukutani chisoni mantha achoke,Musandirole ndisochereKuchokera kwa Inu chakumbali.[M’bale Branham akuyamba kung’ung’uzaChikhulupiriro Changa Chimayang’ana KwaInu—Mkonzi.]

Mphamvu ku mtima wanga wofooka,Kudzoza changu changa;Ingitsani mdima usanduke usana,Pukutani chisoni mantha achoke,O mundirole kuyambira leroNdikhale mwathunthu Wanu!

165 O Yesu, ife tikuwona tiri kuyandikira chinachake. Yesayamneneri anali atayankhula za icho; Yeremia anayankhula zaicho. Daniele anayang’ana mmbuyo ndipo anawona chimeneiwo ankanena. Icho chinapangitsa mtima wake kuti ukhalewokondowezeka, ndipo iye—iye anayang’anitsa nkhope yakecholoza Kumwamba. Iye anasala, ziguduli ndi mapulusa. Iyeankafuna kuti amve, kuti iye angakhoze kuwachenjeza anthu.166 Ambuye, ife tikuwona mwa Mabuku, nafenso, Bukhu Lanu,Bukhu la Yesaya, Bukhu la Yeremia, Bukhu la Yakobo, Yohane,Luka, Marko, Mateyu, Bukhu la Chivumbulutso, MabukuAnu onse, kuti ife tiri pafupi mapeto. Ndipo ife talozetsankhope yathu moyang’anitsa Kumwamba, mu pemphero,mapembedzero, kuti tipeze pamene ife tiri kukhala, Ambuye.Ife tikuyamba kuwona kuwala kwa masana kukusweka.Ndipo, Ambuye, ife tikubwera kwa Inu. Chikhulupirirochathu chikuyang’ana kwa Inu tsopano. Kuika kumbali

Page 47: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

MALANGIZO A GABRIELI KWA DANIELE 47

cholemera chirichonse, tchimo lirilonse, kusakhulupirirakwakung’ono kulikonse komwe kungatifooketse ife mophweka,ife tikulimbikira tsopano kupita ku kuitana kwa pamwamba,podziwa kuti nthawi yathu ili yochepa.167 Adalitseni anthu awa muno, Ambuye. Iwo amakukondaniInu. Iwo ali Anu. Iwo atuluka. NdinuMmodzi yemwemukuchitakuululako. Ife tikupemphera kuti Inu mupereke zinthu izi kwaife pamene ife tikuyembekezera pa Inu.168 Tipatseni ife madzulo abwino a kuphunzira, Ambuye.Tipatseni ife kumvetsa. Tibweretseninso ife kachiwiri usikuuno,mwatsopano. Ambuye, ndidzozeni ine madzulo ano, o, pameneine ndikuwerenga, Ambuye, pofuna cholinga chofutukukapasanu ndi kamodzi ichi cha kudzacheza kwa Gabrieli. NgatiGabrieli anabwera kuti adzacheze ndi kupereka tanthauzolofutukuka pasanu ndi kamodzi, Ambuye, ife tiyenera kudziwazimenezo. Ife tikuphunzira mwa Mabuku ndipo tikudziwa kutiife tiri pafupi. Kotero ife tikupemphera kuti Inumuulule izo kwaife usikuuno.169 Lamlungu lotsatira, Ambuye, O Mulungu, ayikeni masikuamenewo mkati mmenemo. Ine sindikudziwa motani, komaInu mukhoza kutibweretsa ife mpaka ku nthawiyo. Perekaniizo, Atate. Ife tikuyang’ana kwa Inu. Ife timakondana winandi mzake mwa Magazi a Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu,watitsuka ife kuchokera ku tchimo lonse. Ife tikuyang’ana kwaInu tsopano. Tithandizeni ife pamene ife tikuyembekezera paInu, Atate, kupyolera mwa Yesu Ambuye wathu.

Page 48: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele(Gabriel’s Instructions To Daniel)Julaye 30, 1961, Lamlungu m’mawa

Cholinga Chofutukuka Pasanu Ndi KamodziCha Gabrieli Kudzacheza Kwa Daniele

(The Sixfold Purpose Of Gabriel’s Visit To Daniel)Julaye 30, 1961, Lamlungu usiku

Sabata La Makumi Asanu Ndi Chiwiri La Daniele(The Seventieth Week Of Daniel)Ogasiti 6, 1961, Lamlungu m’mawa

Uthenga uwu wa M’bale William Marrion Branham unalalikiridwa ku BranhamTabernacle mu Jeffersonville, Indiana, U.S.A. Titapeza kaye matepi omvekerapondi athunthu kwambiri apachiyambi, bukhu ili la Mawu Oyankhulidwa laMasabata Makumi Asanu Ndi Awiri A Daniele lalembedwanso molingana ndindondomeko yatsopano. Kuyesetsa kulikonse kwapangidwa kuti tisamutsemolondola Uthenga woyankhulidwa kuchokera pa kujambula kwa matepiamaginito kuti zidindidwe pa tsamba, ndipo zatsindikizidwa mkatimumosachotsera mawu ena ndi kugawidwa ndi Voice Of God Recordings.

CHICHEWA

©2001 VGR, ALL RIGHTS RESERVED

VOICE OF GOD RECORDINGS, MALAWI OFFICE

P.O. BOX 51453, LIMBE, MALAWI

VOICE OF GOD RECORDINGS

P.O. BOX 950, JEFFERSONVILLE, INDIANA 47131 U.S.A.www.branham.org

Page 49: CHA61-0730M Malangizo A Gabrieli Kwa Daniele VGRdownload.branham.org/pdf/CHA/CHA61-0730M Gabriels... · 12 Ndipo tsopano, pamene ife tikutembenuzira ku Salmo ili, ine ndiri nazo zolengeza

Chidziwitso kwa ofuna kusindikiza

Maufulu onse ndi osungidwa. Bukhu ili mukhoza ku printa kunyumba kwanu ngati mutafuna kuti mugwiritse ntchito inuyo kapena kuti mukawapatse ena, ulere, ngati chida chofalitsira Uthenga wa Yesu Khristu. Bukhu ili simungathe kuligulitsa, kulichulukitsa kuti akhalepo ambiri, kuikidwa pa intaneti, kukaliika pakuti ena azitengapo, kumasuliridwa mu zinenero zina, kapena kugwiritsidwa ntchito ngati njira yopezera ndalama popanda chilolezo chochita kulembedwa ndi a Voice Of God Recordings®.

Ngati mukufuna kuti mumve zambiri kapena ngati mukufuna zipangizo zina zimene tiri nazo, chonde mulembere ku:

Voice of God RecoRdinGsP.o. Box 950, JeffeRsonVille, indiana 47131 U.s.a.

www.branham.org